Mphu. 49 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 2Maf. 22.1; 22.11-13; 23.3, 25 Kukumbukira za Yosiya kuli ngati kumva

zonunkhira zokoma,

monga lubani wosakanizidwa bwino ndi mmisiri.

Kuli ngati kutsekemera kwa uchi pa khosi,

ndiponso ngati nyimbo yoimba pa phwando la vinyo.

2Adatsata njira yabwino ya kutembenuza mitima ya anthu,

ndipo adachotsa zonyansa zonse za mafano.

3Adakhala wokhulupirika kwathunthu kwa Ambuye,

ndipo adalimbitsa chipembedzo choona pa nthaŵi

ya chisokonezo choipa.

Yeremiya

4Mafumu onse anali ochimwa kupatula Davide,

Hezekiya ndi Yosiya.

Poti adasiya Malamulo a Wopambanazonse,

mafumu a ku Yuda adatha.

5Adapereka ulamuliro wao kwa anthu ena,

ndi ulemerero wao kwa anthu achilendo.

6 Yer. 1.4-10; 39.8 Anthu ameneŵa adatentha mzinda wosankhidwa,

malo opembedzerapo.

Adasiya miseu yake popanda anthu, monga momwe

Yeremiya adaanenera.

7Anthu adamzunza Yeremiya,

mneneri amene Mulungu adampatula akali m'mimba

mwa mai wake kuti azule ndi kugwetsa, aononge ndi kugumula,

komanso kuti amange ndi kubzala.

Ezekiele

8 Ezek. 1.3-15; 14.14-20 Ezekiele adaona ulemerero wa Mulungu m'masomphenya,

umene Mulungu adamuwonetsa pamwamba pa galeta la Akerubi.

9Ambuye adakumbukira adani ake,

naŵatumizira mvula yanamondwe,

koma onse amene anali olungama,

adaŵachitira zabwino.

10Kunena za aneneri khumi ndi aŵiri aja,

mafupa ao akhalenso ndi moyo watsopano kuchokera

ku manda ao,

poti aneneriwo adaika mtima watsopano mwa Yakobe,

ndipo adapulumutsa anthu chifukwa cha chikhulupiriro chao.

Zerubabele ndi Yoswa

11 Eza. 3.2; Hag. 2.23 Kodi Zerubabele tizimtamanda bwanji?

Anali ngati mphete yosindikizira ku dzanja lamanja la Ambuye.

12 Hag. 1.1, 12 Chimodzimodzinso Yoswa, mwana wa Yehozadaki.

Ameneŵa pa nthaŵi yao adamanga Nyumba ya Mulungu,

adamanga Nyumba yoyera ya Ambuye,

Nyumba yoyenera ulemerero wamuyaya.

Nehemiya

13 Neh. 6.15 Mbiri ya Nehemiya njaikulu.

Iye adautsanso zipupa zogamuka za Yerusalemu.

Adamanga zipata ndi mipiringidzo yake

ndi kumanganso nyumba zathu zoonongeka.

Atsogoleri ena

14Palibe wina pa dziko lapansi amene adalengedwa

wolingana ndi Enoki,

chifukwa iye adatengedwa kuchoka pa dziko lapansi.

15Sadabadwepo munthu wina wolingana ndi Yosefe.

Anali mtsogoleri wa abale ake

ndiponso mchirikizi wa anthu ake.

Mafupa ake omwe adaŵasamala mwaulemu.

16Semu ndi Seti adalemekezeka pakati pa anthu,

koma Adamu adapambana zolengedwa zonse zamoyo

pa dziko lapansi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help