Ntc. 26 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Paulo adziteteza pamaso pa mfumu Agripa

1Agripa adauza Paulo kuti, “Tikukulola kuti unene mau ako.” Tsono Paulo adatambalitsa dzanja lake nayamba kunena nkhani yake. Adati,

2“Inu Mfumu Agripa, ine ndikuganiza kuti ndine wamwai kuti ndi pamaso panu pamene ndiyankhe lero zonse zimene Ayuda akhala akundineneza.

3Makamaka chifukwa inu mumaidziŵa bwino miyambo yonse yachiyuda, ndiponso mikangano yao yonse, ndikukupemphani kuti mundimvere moleza mtima.

4“Ayuda onse akudziŵa za moyo wanga wonse kuyambira ndili mwana. Akudziŵa m'mene ndinkakhalira chiyambire pakati pa anthu a mtundu wanga, ndiponso ku Yerusalemu.

5 wekha ngati ng'ombe yoponda zidyali pa chobayira.’

15Apo ndidafunsa kuti, ‘Ndinu yani, Ambuye?’ Ambuyewo adati, ‘Ine ndiye Yesu, amene ukumzunza.

16Koma dzuka, imirira. Pakuti ndakuwonekera kuti ndikuike kuti ukhale mtumiki wanga ndi mboni yanga. Ndifuna kuti ukhale mboni ya m'mene wandiwonera lero, ndiponso ya zimene ndidzakuwonetsa m'tsogolo.

17Ndidzakulanditsa kwa anthu a mtundu wako, ndiponso kwa anthu a mitundu ina kumene ndikukutuma.

18Ndikukutuma kuti anthu ameneŵa uŵatsekule maso, kuti atembenuke kuchoka mu mdima wa machimo nkuloŵa m'kuŵala, ndiponso kuchoka m'mphamvu ya Satana nkutsata Mulungu. Ndifuna kuti akhulupirire Ine, kuti machimo ao akhululukidwe, ndipo alandire nao madalitso pamodzi ndi anthu amene Mulungu adaŵasankha kuti akhale akeake.’

Paulo afotokoza za ntchito yake

19“Nchifukwa chake, mfumu Agripa, sindidakane kumvera zimene Mulungu adandiwonetsa m'masomphenyazo.

20Ntc. 9.20, 28, 29Koma ndidalalika poyamba kwa anthu a ku Damasiko ndi a ku Yerusalemu, ndipo bwino lake ku dziko lonse la Yudeya, ndiponso kwa anthu a mitundu ina. Ndidalalika kuti atembenuke mtima, kutembenukira kwa Mulungu, ndi kuchita ntchito zotsimikiza kuti atembenukadi mtima.

21Chifukwa cha zimenezi Ayuda adandigwira m'Nyumba ya Mulungu nafuna kundipha.

22Koma Mulungu wakhala akundithandiza mpaka lero. Motero ndaimirira pano kuti ndichite umboni pamaso pa anthu onse, aakulu ndi ang'ono omwe. Zimene ndikuŵauza si zina ai, koma ndi zomwezo zimene aneneri ndi Mose adanena kuti zidzachitika.

231Ako. 15.20; Yes. 42.6; 49.6Paja iwo adati Mpulumutsi wolonjezedwa uja adzamva zoŵaŵa, ndipo popeza kuti Iye adzakhala woyamba kuuka kwa akufa, adzalengeza Ayuda ndi amene sali Ayuda za kuŵala kwa chipulumutso.”

Paulo ayankha Fesito ndi Agripa

24Pamene Paulo ankadziteteza ku zomnenezazo, Fesito adanena mokweza mau kuti, “Misalatu imeneyi, iwe Paulo! Kuphunziritsa kwako kukukupengetsa.”

25Koma Paulo adati, “Pepani, a Fesito olemekezeka, sindine wamisala ai. Zimene ndikunenazi nzoona ndi zanzeru.

26Mfumu Agripa akudziŵa zonsezi, nkuwona ndikulankhula pamaso pao momasuka. Ndikhulupirira kuti palibe kanthu nkamodzi komwe pa zimenezi kamene iwo sakadziŵa. Pakuti sizidachitike mobisika ai.

27Inu mfumu Agripa, kodi mumakhulupirira mau a aneneri? Ndikudziŵa kuti mumaŵakhulupirira.”

28Apo Agripa adauza Paulo kuti, “Uganiza kuti nkundisandutsa mkhristu pa kanthaŵi kochepa, komweka?”

29Paulo adati, “Kaya ndi pa kanthaŵi kochepa kaya nthaŵi yaitali, Mulungu akadalola kuti osati inu nokha, komanso anthu onse amene alikumva mau anga lero, akhale monga momwe ndiliri inemu, kupatula maunyolo okhaŵa.”

30Pamenepo mfumu Agripa, bwanamkubwa, Berenise, ndi onse amene anali nawo adaimirira.

31Atachokapo adauzana kuti, “Munthuyu sakuchita chilichonse choyenera kumuphera kapena kumponyera m'ndende.”

32Tsono Agripa adauza Fesito kuti, “Tikadammasula munthuyu akadapanda kupempha kuti mlandu wakewu ukazengedwe ndi Mfumu ya ku Roma.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help