Yob. 16 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yobe

1Yobe adayankha kuti,

2“Zoterezi ndidazimva kale.

Nonsenu ndinu anthu osatha kuthuzitsa mtima mnzanu.

3Kodi mudzakhala mukulankhulabe

mau achabechabeŵa mpaka liti?

Kaya chakuvutani nchiyani

kuti muzilankhulabe mau otsutsaŵa?

4Inenso ndikadalankhula monga inu,

mukadakhala monga ndiliri inemu.

Inenso ndikadatha kulankhula monga mukulankhuliramu.

Nanenso ndikadakupukusirani mutu.

5Ndikadakulimbitsani ndi mau anga,

ndikadakuthuzitsani mtima ndi kuchepetsa zoŵaŵa zanu.

6“Ine ndikati ndilankhule, zoŵaŵa zanga sizichepa.

Ndikati ndikhale chete, zoŵaŵazo zikhala zilipobe.

7Ndithudi, Mulungu wanditha mphamvu,

waononga banja langa lonse.

8Wandigwira, ndipo wasanduka mdani wanga,

umboni woti ndine wolakwa. Ndatsala mafupa okhaokha,

ndipo chimenechi chikunditsimikiza kuti ndine wolakwa.

9Mulungu wanding'amba ali chikwiyire,

ndipo akudana nane, wachita kulumira mano.

Mdani wanga akundituzulira maso.

10Anthu amandinyoza polankhula,

amandimenya pa tsaya mwachipongwe,

akundichitira upo kuti alimbane nane.

11Mulungu wandipereka kwa anthu osasamala za Iye,

wandiponya m'manja mwa anthu oipa.

12Ndidaali pa mtendere,

koma Mulungu adanditswanya.

Adandigwira pa khosi ndi kundiphwanya.

Adandiimika kuti ndikhale choponyerapo chandamale chake.

13Mivi yake ikundilasa pa mbali zonse.

Walasa impso zanga mopanda chifundo,

watayira pansi ndulu yanga.

14Akundivulazavulaza.

Akulimbana nane ngati munthu wankhondo.

15“Ndasokerera chiguduli pathupi panga.

Ndaika mphamvu zanga pa fumbi.

16Maso anga afiira nkulira,

ndipo zikope zanga zatupa kwambiri.

17Koma sindidachite chiwawa chilichonse,

pemphero langa kwa Mulungu ndi lolungama.

18“Iwe, dziko lapansi, usabise zoipa zimene andichita.

Kulira kwanga kofuna thandizo kusalekeke.

19 Yob. 19.25 Tsopano lino mboni yanga ili kumwamba,

wonditchinjiriza ali komweko.

20Abwenzi anga akundinyodola,

choncho ndikulirira kwa Mulungu.

21Kukadapezeka wondipepesera kwa Mulungu,

bwenzi atandipepesera,

monga momwe munthu amachitira mnzake.

22Pakuti zitapita zaka pang'ono,

ndidzayenda njira imene sindidzabwerera.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help