1 Mt. 5.31; 19.7; Mk. 10.4 Tiyese kuti munthu wakwatira mkazi, pambuyo pake nkunena kuti mkaziyo sakumfuna, chifukwa choti wampeza cholakwa. Alembe kalata yachisudzulo, ndi kumpatsa mkaziyo pamanja, namchotsa pakhomo pake.
2Mkaziyo akakwatiwa ndi mwamuna wina,
3ndipo pambuyo pake winayonso nkunena kuti sakumfuna, angathe kumlemberanso kalata yachisudzulo nkumpatsa. Mkaziyo atachokapo pakhomopo, kapena mwamuna wachiŵiri uja atafa,
4mwamuna wake woyamba uja sayenera kumkwatiranso, ayenera kumuwona ngati woipitsidwa. Kumkwatiranso nkuchimwa pamaso pa Chauta. Tsono musaloŵemo ndi cholakwa m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo.
Malamulo osiyanasiyana5Munthu akangokwatira kumene, musamlembe m'gulu la ankhondo, kapena kumpatsa ntchito ina iliyonse. Papite chaka chathunthu asanachite zimenezi, kuti choncho athe kukhala kwao ndi kumakondweretsa mkazi wake amene adamkwatirayo.
6Mukakongoza munthu kanthu, musamtengere mphero yake yoperera tirigu kuti ikhale pinyolo. Kumlanda chimenechi, ndiye kumchotsera chinthu chomuthandiza pa moyo wake.
7 Eks. 21.16 Aliyense woba Mwisraele mnzake ndi kumsandutsa kapolo kapena kumgulitsa ngati kapolo, aphedwe ndithu. Motero mudzachotsa choipa chimenechi pakati pa inu.
8 Lev. 13.1—14.54 Kunena za nthenda ya khate, muwone ndithu kuti mukutsatadi malangizo onse amene ndapatsa ansembe Achilevi, ana a Levi, kuti akuuzeni.
9Num. 12.10 Kumbukirani zimene Chauta, Mulungu wanu, adamchita Miriyamu, muja munkachokera ku Ejipitomu.
10 Eks. 22.26, 27 Mukakongoza munthu kanthu, musaloŵe m'nyumba mwake kukatenga chovala chimene afuna kukupatsani ngati pinyolo.
11Inu mukhale panja, mwini wakeyo achite kukupatsani yekha.
12Ngati munthuyo ndi wosauka, chovala chapinyolocho chisakagone kwanu.
13Chibwezeni dzuŵa lisanaloŵe, kuti iye afunde usiku. Apo adzakuthokozani, ndipo Chauta, Mulungu wanu, adzakondwera nanu.
14 Lev. 19.13 Wantchito wolembedwa amene ali mmphaŵi ndi wosoŵa, musamamdyerera, ngakhale akhale mnansi wanu kapena mlendo wokhala mumzinda mwanu m'dziko lanulo.
15Tsiku lililonse dzuŵa lisanaloŵe, muzimlipira malipiro a tsikulo. Ndalamazo akuzisoŵa iyeyo ndipo akuŵerengera zomwezo. Mukapanda kumlipira, adzakulirirani kwa Mulungu ndipo mudzatsutsidwa kuti ndinu ochimwa.
16 2Maf. 14.6; 2Mbi. 25.4; Ezek. 18.20 Makolo asafere zolakwa za ana ao. Momwemonso ana asafere zolakwa za makolo ao. Munthu aphedwe chifukwa cha zoipa za iye mwini.
17 Eks. 23.9; Lev. 19.33, 34; Deut. 27.19 Alendo kapena ana amasiye musaŵalande zao zoŵayenera, poŵapotozera mlandu wao. Ndipo mkazi wamasiye musamlande chovala kuti chikhale pinyolo ya ngongole.
18Kumbukirani kuti paja mudaali akapolo ku Ejipito, ndipo kuti Chauta, Mulungu wanu, adakuwombolani kumeneko. Nchifukwa chake ndakupatsani lamulo limeneli.
19 Lev. 19.9, 10; 23.22 Mukamakolola dzinthu m'minda mwanu, zina pang'ono nkuiŵalika, musabwerere kukatenga zoiŵalikazo. Zimenezo muzisiyire alendo okhala nanu, ana amasiye ndi akazi amasiye, ndipo Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse.
20Mutatha kukolola olivi koyamba, musapitemonso m'mitengomo kukatenga zotsala. Zimenezo ndi za alendo okhala nanu, za ana amasiye ndi akazi amasiye.
21Mutha kuthyola koyamba mphesa zanu, koma musapitemonso kachiŵiri m'mitengomo. Mphesa zotsalazo ndi za alendo okhala nanu, za ana amasiye ndi akazi amasiye.
22Mukumbukire kuti mudaali akapolo m'dziko la Ejipito. Nchifukwa chake ndakupatsani lamulo limeneli.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.