1Koma mizimu ya anthu olungama
ili m'manja mwa Mulungu
ndipo masautso sadzaigwera konse.
2 Lun. 4.17 Pamaso pa anthu opusa,
ankaoneka ngati adafa,
ndipo imfa yao inkaoneka ngati
tsoka lalikulu.
3Kutisiya kwaoko kunali ngati kuwonongekeratu,
pamene eniakewo ali pa mtendere.
4Ngakhale pamaso pa anthu
ankaoneka ngati olangidwa,
koma eniake anali ndi chikhulupiriro chosatha.
5 Aro. 8.18; 2Ako. 4.17 Atalangidwa pang'ono,
adzaona madalitso aakulu,
chifukwa Mulungu ankangoŵayesa,
ndipo adaŵapeza kuti ndi oyenera kukhala naye.
6Adaŵayesa ngati golide m'ng'anjo ya moto,
ndipo adaŵavomera
monga momwe amavomerera nsembe zopsereza.
7Mulungu akadzaŵayendera, iwowo adzaŵala,
ndipo adzathamanga monga amachitira
malaŵi a moto pakati pa udzu wouma.
8Iwo adzaweruza mitundu ya anthu
ndi kulamulira anthu onse,
ndipo Ambuye adzakhala mfumu yao mpaka muyaya.
9Amene amamukhulupirira adzamvetsa zoona,
ndipo amene amalimbikira adzakhala naye m'chikondi chake,
chifukwa Iye amachitira ufulu ndi chifundo
anthu ake osankhidwa.
10Koma anthu osamvera Mulungu,
amene adanyoza munthu wolungama, naukira Ambuye,
adzalandira chilango molingana ndi maganizo ao oipawo.
11Pajatu anthu onyoza nzeru ndi mwambo ali ndi tsoka.
Chikhulupiriro chao ndi chopandapake,
ntchito zao ndi zachabechabe,
kukangalika kwao nkopanda ntchito,
zochita zao nzopanda phindu.
12Anthu otere akazi ao ndi opusa,
ana ao ndi oipa kwambiri,
zidzukulu zao nzotembereredwa.
Ndi bwino kukhala wosabala koma uli wachilungamo13Nchifukwa chake ngwodala mkazi wosabereka,
amene ali woyera mtima,
ndipo sadachimwepo ndi amuna.
Adzakhala ndi zipatso
pamene Mulungu adzaweruza mizimu.
14Ngwodalanso mwamuna wofulidwa,
amene manja ake sadachite zoipa,
ndi amene sadaganize zochimwira Ambuye.
Ameneyo adzalandira mphotho yapadera
chifukwa cha kukhulupirika kwake,
ndipo adzapeza malo okondweretsa kwambiri
m'Nyumba ya Ambuye.
15Ntchito zabwino zotsatira zake ndi ulemerero,
luntha lili ngati muzu wamoyo
umene sulephera kuphukira.
16Koma ana a anthu achigololo sadzalimba,
ana a ukwati wosayenera adzazimirira.
17Ngakhale moyo wao ukhale wa zaka zambiri,
adzaŵayesa anthu achabechabe,
potsiriza, ukalamba wao sudzalemekezeka.
18Ngati afa akali achinyamata,
adzakhala opanda chikhulupiriro
ndi osasangalala pa tsiku la mlandu,
19chifukwa mtundu wosalungama
umatha moopsa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.