Yob. 37 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Nanenso ndimaopa zazikuluzi,

mtima wanga umalumphalumpha kuchoka m'malo mwake.

2Mumvetsetse kulira kwa liwu la Mulungu,

ndiye kuti kugunda kotuluka m'kamwa mwake.

3Amaponya ching'aning'ani pansi pa thambo,

kuŵala kwake kumafika ku ngodya zonse za dziko lapansi.

4Pambuyo pake kugunda kwa Mulungu kumamveka,

amagunda ndi liwu lake lalikulu

pamene mphezi zikung'anipa.

5Mulungu amachita zodabwitsa ndi liwu lake.

Amachita zazikulu zimene sitingathe kumvetsa.

6Amalamula chisanu chambee kuti

chigwe pa dziko lapansi.

Amalamulanso mvula kuti igwe mwamphamvu.

7Pamenepo Mulungu amalepheretsa

anthu kugwira ntchito zao.

Motero iwowo amazindikira kuti

Iye mwini ali pa ntchito.

8Pomwepo zilombo zimathaŵira ku michembo yake,

ndipo zimakabisalira m'ngaka zake.

9Kamvulumvulu amakuntha kuchokera ku malo ake,

mphepo imadzetsa chisanu chambiri.

10Mpweya wa Mulungu umaunditsa chisanu,

ndipo madzi am'nyanja amauma kuti gwa.

11Mitambo yochindikira amaidzaza ndi madzi a mvula,

ndipo amabalalitsa zing'aning'ani kuchokera m'mitambo.

12Mulungu amayendetsa mitambo mozungulirazungulira,

kuti ichite zonse zimene Iye akufuna pa dziko lapansi.

13Mwina amagwetsa mvula pansi pano kuti ikhale chilango,

mwina kuti aonetse chikondi kwa anthu,

pothirira nthaka yao.

14“Inu aYobe, tamvani izi,

imani, muganizire ntchito zodabwitsa za Mulungu.

15Kodi mukudziŵa m'mene Mulungu amazichitira,

ndi m'mene amang'anipitsira mphezi m'mitambo yake?

16Kaya mukudziŵa m'mene Mulungu amayalira mitambo,

ntchito yosonyeza nzeru zake zodabwitsa,

17paja inu zovala zanu mumamva kutentha kwambiri

pamene mphepo yakumwera ikuwomba pa dziko?

18Kodi mungathe kufanafana naye Mulungu

amene adatambasula thambo

lili lolimba ngati chitsulo?

19“Chabwino, tiphunzitsenitu zoti tidzamuuze.

Ifeyo sitingathe kunena kanthu

poti mwa ife mwachita mdima.

20Kodi nkofunikira kumdziŵitsa

Mulungu kuti ndili naye ndi mau?

Kodi kutero si kuchita ngati kupempha kuti ndiwonongeke?

21“Tsopano anthu sangathe kuyang'anitsitsa kuŵala,

pamene kukunyezimira kwambiri mu mlengalenga,

pamene mphepo yaomba nkuchotsa mitambo yonse.

22Kuŵala kwake kumaonekera chakumpoto.

Mulungu amaonetsa ulemerero woopsa.

23Mphambe sitingathe kumufika pafupi,

ndi woopsa pa ulamuliro ndi pa mphamvu.

Ndi wolungamadi kwambiri, sangazunze anthu.

24Nchifukwa chake anthu amamuwopa kwambiri.

Iye sasamalako wina aliyense

amene amadzinyenga kuti ndi wanzeru.”

Chauta alankhula.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help