1 Pet. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za mwala wamoyo

1Nchifukwa chake tayani choipa chonse, kunyenga konse, chiphamaso, kaduka ndi masinjiriro onse.

2Monga makanda obadwa chatsopano amalirira mkaka, inunso muzilakalaka mkaka weniweni wodyetsa mtima wanu, kuti ukukuzeni ndi kukufikitsani ku chipulumutso,

3Mas. 34.8 popeza kuti mwachilaŵadi chifundo cha Ambuye.

4Bwerani kwa Iye amene ali mwala wamoyo womwe anthu adaukana, koma Mulungu adausankha kuti ngwamtengowapatali.

5Inunso mukhale ngati miyala yamoyo yoti Mulungu amangire nyumba yake. M'menemo muzitumikira ngati ansembe opatulika, pakupereka nsembe zochokera ku mtima, zokomera Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu.

6Yes. 28.16Paja m'Malembo mudalembedwa kuti.

“Ndasankha mwala wamtengowapatali.

Ndikuuika tsopano m'Ziyoni, ngati mwala wapangodya.

Wokhulupirira Iye sadzachita manyazi.”

7 Mas. 118.22 Tsono kwa inu okhulupirira, Iye ndi wamtengowapatali. Koma kwa osakhulupirira, ndi monga momwe mau a Mulungu anenera kuti,

“Mwala womwe amisiri omanga nyumba adaukana,

womwewo wasanduka mwala wapangodya.”

8 Yes. 8.14, 15 Mau a Mulungu akutinso,

“Umenewu ndi mwala wokhumudwitsa anthu,

ndi thanthwe loŵagwetsa.”

Amakhumudwa popeza kuti amakana kumvera mau a Mulungu, ndipo anali oyeneradi kuti adzaone zotere.

Za mtundu wosankhidwa

9 Eks. 19.5, 6; Yes. 43.20; Eks. 19.5; Deut. 4.20; 7.6; 14.2; Tit. 2.14; Yes. 43.21; Yes. 9.2 Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.

10Hos. 2.23Kale simunali anthu a Mulungu, koma tsopano ndinu anthu ake. Kale simudaalandira chifundo, koma tsopano mwachilandira.

11Okondedwa anga, popeza kuti ndinu alendo pansi pano, ndikukupemphani kuti musagonjere zilakolako zathupi zimene zimachita nkhondo ndi mzimu wanu.

12Samalani mayendedwe anu pakati pa akunja, kuti ngakhale azikusinjirirani kuti ndinu anthu ochita zoipa, komabe aziwona ntchito zanu zabwino. Apo adzalemekeza Mulungu pa tsiku limene Iye adzaŵayendere.

13Chifukwa cha Ambuye, muzimvera akulu onse olandira ulamuliro. Ngati ndi mfumu yaikulu koposa ija, imvereni chifukwa ili ndi ulamuliro pa mafumu ena onse.

14Ngati ndi nduna, zimvereni chifukwa zidachita kutumidwa ndi mfumu kuti zizilanga ochita zoipa ndi kuyamikira ochita zabwino.

15Paja Mulungu amafuna kuti ndi zochita zanu zabwino muthetse kulankhula kosadziŵa kwa anthu opusa.

16Inde muzikhala ngati mfulu, koma ufulu wanuwo usakhale ngati chinthu chophimbira zoipa. Koma khalani ngati atumiki a Mulungu.

17Muzilemekeza anthu onse. Muzikonda akhristu anzanu. Khalani anthu oopa Mulungu. Mfumu yaikulu koposa ija muziipatsa ulemu.

Chitsanzo cha Khristu womva zoŵaŵa

18Inu antchito, muzimvera ndi ulemu wonse anthu okulembani ntchito, osati okhawo amene ali abwino ndi ofatsa ai, koma ndi ovuta omwe.

19Pajatu ndi chinthu chabwino ngati munthu, chifukwa chokumbukira Mulungu, apirira zoŵaŵa zosamuyenera.

20Kodi pali chiyani choti nkukuyamikirani ngati mupirira pamene akumenyani chifukwa choti mwachimwa? Koma mukapirira zoŵaŵa mutachita zabwino, apo mwachita chinthu chovomerezedwa ndi Mulungu.

21Mkhalidwe wotere ndi umene Mulungu adakuitanirani. Paja Khristu nayenso adamva zoŵaŵa chifukwa cha inu, nakusiyirani chitsanzo kuti muzilondola mapazi ake.

22Yes. 53.9Iye sadachitepo tchimo lililonse, ndipo sadanene bodza lililonse.

23Yes. 53.7Pamene anthu ankamuchita chipongwe, Iye sadabwezere chipongwe. Pamene ankazunzika, Iye sadaopseze, koma adapereka zonse kwa Mulungu amene amaweruza molungama.

24Yes. 53.5, 6Khristu mwiniwake adasenza machimo athu m'thupi lake pa mtanda, kuti m'machimo tikhale ngati akufa, koma pakutsata chilungamo tikhale amoyo ndithu. Mudachiritsidwa ndi mabala ake.

25Munali ngati nkhosa zosokera, koma tsopano mwabwerera kwa Mbusa amene ndi wokuyang'anirani.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help