Mas. 103 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za chikondi cha MulunguSalmo la Davide.

1Tamanda Chauta, iwe mtima wanga,

moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera.

2Tamanda Chauta, iwe mtima wanga,

ndipo usaiŵale zabwino zake zonse.

3Ndiye amene amakhululukira machimo ako onse,

ndi kuchiritsa matenda ako onse.

4Ndiye amene amapulumutsa moyo wako ku manda.

Amakuveka chikondi chake chosasinthika

ndiponso chifundo chake ngati chisoti chaufumu.

5Ndiye amene amakupatsa zabwino

nthaŵi zonse za moyo wako,

choncho umakhalabe wa mphamvu zatsopano ngati mphungu.

6Chauta amaweruza mwachilungamo onse opsinjidwa

amaŵachitira zolungama.

7Adadziŵitsa Mose njira zake,

adaonetsa Aisraele ntchito zake.

8 Yak. 5.11 Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima,

ndi wosakwiya msanga,

ndipo chikondi chake chosasinthika nchachikulu.

9Akatikalipira,

mkwiyo wake sudzakhala woyaka mpakampaka.

10Satilanga moyenerera machimo athu,

satibwezera molingana ndi zolakwa zathu.

11Monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi,

ndi momwenso chidakulira chikondi chake chosasinthika

kwa anthu oopa Chauta.

12Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe,

ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu

kuti zikhale kutali ndi ife.

13Monga bambo amachitira chifundo ana ake,

ndi momwenso Chauta amaŵachitira chifundo omulemekeza.

14Amadziŵa m'mene adatipangira,

amakumbukira kuti ife ndife fumbi.

15Kunena za munthu, masiku ake sakhalitsa,

ali ngati a udzu,

munthuyo amakondwa ngati duŵa lakuthengo.

16Koma mphepo ikaombapo, duŵalo pamakhala palibe,

siliwonekanso pa malo ake.

17Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya

kwa anthu omumvera,

zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama.

18Anthuwo ndi amene amasunga chipangano chake,

amene amakumbukira kusunga malamulo ake.

19Chauta wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba,

ndipo amalamulira zonse mu ufumu wake.

20Tamandani Chauta, inu angelo ake,

inu amphamvu amene mumamva mau ake,

amene mumachita zimene amalamula.

21Tamandani Chauta, inu magulu a ankhondo ake onse,

atumiki ake ochita zimene Iye afuna.

22Tamandani Chauta, inu zolengedwa zake zonse,

ku madera onse a ufumu wake.

Nawenso mtima wanga, tamanda Chauta!

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help