Mas. 67 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nyimbo yothokozaKwa Woimbitsa Nyimbo. Salmo loimbira zipangizo zazingwe. Nyimbo.

1Inu Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa,

mutiwunikire ndi chikondi chanu,

2Njira yanu idziŵike pa dziko lonse lapansi,

chipulumutso chanu chidziŵike pakati pa mitundu yonse.

3Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu,

mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni.

4Mitundu ya anthu isangalale ndi kuimba ndi chimwemwe,

chifukwa Inu mumaweruza anthu mwachilungamo,

ndi kuŵatsogolera pa dziko lapansi.

5Mitundu yonse ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu,

mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni.

6Nthaka yabereka zipatso zake,

Mulungu, Mulungu wathu watidalitsa.

7Inde, Mulungu watidalitsa,

anthu onse a ku mathero a dziko lapansi apembedze Iye.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help