1 Miy. 2.6 Nzeru zilizonse nzochokera kwa Ambuye,
zimakhala ndi Iwo nthaŵi zonse.
2Ndani angaŵerenge mchenga wakunyanja?
Ndani angaŵerenge madontho a mvula?
Ndipo ndani angaŵerenge masiku a muyaya?
3Ndani angathe kuyesa kutalika kwa mlengalenga?
Ndani angayese kukula kwa dziko lapansi?
Ndani angayese kuzama kwa phompho?
Nanji tsono ndani angayese kuzama kwa nzeru?
4Nzeru ndizo zinali zoyamba kulengedwa,
zinthu zina zilizonse zisanalengedwe.
Kumvetsa zinthu mwanzeru kudaalipo chiyambire.
5Kasupe wa nzeru ndi mau a Mulungu
amene ali kumwamba.
Makhalidwe ake ndi malamulo amuyaya.
6Maziko a nzeru ndani adamuululirapo?
Nanga kuchenjera kwake ndani amakudziŵa?
7Ndani amadziŵa zonse zimene nzeru zimadziŵa?
Ndani amamvetsa zonse zimene nzeru zimamvetsa?
8Alipo Mmodzi yekha wanzeru,
woyenera kumamuwopa kwambiri,
wokhala pa mpando wake waufumu.
Ameneyo ndi Ambuye.
9 Miy. 8.22-31; Mphu. 24.9 Ndiwo amene adalenga nzeru,
adaziyang'ana ndi kuziyesa
ndipo adaziika m'ntchito zake zonse.
10Nzeruzo zimakhala mwa anthu
ngati mphatso ya Mulungu,
ndipo Iyeyo amazipatsa amene amamkonda.
Za Kuwopa Mulungu11Kuwopa Ambuye kumapatsa ulemerero
ndi chikondwerero,
kumapatsa chimwemwe
ndi nsangamutu ya chisangalalo.
12Kuwopa Ambuye kumakondweretsa mtima,
kumapatsa chisangalalo,
chimwemwe ndi moyo wautali.
13Amene amaopa Ambuye,
zonse zidzamuyendera bwino mpaka ku mathero.
Mulungu adzamdalitsa pa tsiku la kufa kwake.
14Kuwopa Ambuye ndiye chiyambi cha nzeru.
Anthu okhulupirika amazilandira
akali m'mimba mwa amai ao.
15Zimakhazikika pakati pa anthu mpaka muyaya,
ndipo zidzukulu za anthuwo
zidzadalira nzeru zimenezo.
16Kuwopa Ambuye ndiye nzeru zenizeni,
anthu amakhuta ndi zipatso zake.
17 Lun. 7.11 Nzeru zimadzaza nyumba za anthu
ndi zimene iwo akufuna,
nkhokwe zao zimadzaza ndi zokolola zake.
18Kuwopa Ambuye ndiye nzeru zonse zathunthu,
kumapatsa mtendere ndi moyo wamphamvu.
19Nzeru zimathandiza kudziŵa
ndi kumvetsa zinthu.
Onse amene ali nazo nzeruzo,
zimaŵakulitsira ulemerero wao.
20 Miy. 3.16; 4.10 Kuwopa Ambuye ndiye maziko a nzeru,
nthambi zake ndi moyo wautali.
21Kuwopa Ambuye kumachotsa machimo;
pamene nzeru zakhazikika,
mkwiyo umathaŵapo.
22Kukwiya popanda chifukwa
sikungakhale chinthu cholungama.
Mkwiyo umaononga mwiniwake yemwe.
23Munthu wopirira amadzigwira
mpaka nthaŵi yake yoyenera itafika,
pambuyo pake amadzakondwera kwabasi.
24Mau ake amaŵasunga mu mtima,
mpaka nthaŵi yake itafika.
Pambuyo pake anthu amadzakamba
zoti munthuyo ngwanzeru.
25Nzeru zili ndi malangizo okhwima
m'nkhokwe mwake,
koma kukonda zachipembedzo
munthu woipa kumamunyansa.
26Ukafuna nzeru, tsata malamulo,
apo Ambuye adzakupatsadi nzeruzo.
27Kuwopa Ambuye
ndiye nzeru ndi kusunga mwambo.
Kukhulupirika ndi kufatsa
ndiye zimene zimakondweretsa Ambuyewo.
28Usanyozere za kuwopa Ambuye,
usaŵayandikire Ambuyewo ndi mtima wonyenga.
29Usakhale wachiphamaso pakati pa anthu,
ndipo uzisamala bwino mau ako.
30Usadzitame kuwopa kuti ungagwe nuchita manyazi,
Ambuye nkuulula zinsinsi zako
ndi kukuchititsa manyazi pamaso pa anthu,
chifukwa mayendedwe ako sanali oopa Ambuyewo.
Mtima wako unali wonyenga kwambiri.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.