1Inu a ku Ninive,
othira nkhondo akubwera kudzakuwonongani.
Ikani ankhondo pa malinga!
Muziyang'ana ku mseu!
Konzekerani nkhondo!
Valani dzilimbe!
2Patsala pang'ono kuti Chauta
abwezere ulemerero wa Israele,
monga udaaliri kale,
ofunkha asanalande zinthu zonse
ndi kuwononga mphesa zao.
3Zishango za ankhondo ao nzofiira,
asilikali ao onse avala zovala zamlangali.
Atandanda pa mizere yankhondo,
magaleta ao akuchezimira ngati malaŵi a moto.
Akavalo akungoti jodojodo.
4Magaleta akuthamanga m'miseu.
Ali piringupiringu m'mabwalo.
Ali ŵaliŵali ngati miyuni yoyaka.
Ali ng'aning'ani ngati mphezi.
5Atsogoleri a ankhondo akuitanidwa,
akubwera naphunthwa.
Akuthamangira ku linga la mzinda,
akuimika chipupa chodzitetezera.
6Akutsekula zipata zotchinga dziŵe la madzi,
kunyumba kwa mfumu kwadzaza mantha.
7Mfumukazi yake yatengedwa ukapolo.
Adzakazi ake akulira ngati nkhunda,
ndipo akudzigunda pa chifuwa.
8Ninive wasanduka ngati chidziŵe,
chimene madzi ake ali faa kutuluka.
Ena akufuula kuti, “Imani! Imani!”
Koma palibe amene akubwerera.
9Funkhani siliva!
Funkhani golide!
Chuma chake nchosatha,
za mtengo wapatali nzosaŵerengeka.
10Mzinda wa Ninive waonongeka,
wasanduka bwinja, wopanda anthu.
Mitima yachokamo, maondo akuwombana,
m'nkhongono muli zii,
nkhope zasinthika ndi mantha.
11Kodi tsopano mzinda uja uli kuti?
Unali ngati phanga la mikango,
m'mene ana ake ankadyeramo,
m'mene mikango yonse inkakhala mopanda mantha.
12Mkango wamphongo unkapha nyama
yokwanira mkango waukazi ndi ana ake.
Unkadzaza phanga lakelo ndi nyama yokadzulakadzula.
13Chauta Wamphamvuzonse akuuza a ku Ninive kuti,
“Ine sindikugwirizana nanu,
ndidzakutentherani magaleta anu.
Lupanga lidzakuwonongerani ankhondo anu
amene ali ngati mikango.
Ndidzakulandani zonse
zimene mudafunkha pa dziko lapansi.
Amithenga anu sadzamvekanso mau.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.