1Mwina mneneri kapena womasulira maloto adzaoneka pakati panupo, namanena kuti adzachita chizindikiro kapena chozizwitsa,
2Chizindikirocho kapena chozizwitsacho chikachitikadi, iye nakuuzani kuti mupembedze ndi kutumikira milungu ina imene simudaipembedzepo nkale lonse,
3inu musamvere zimenezo. Chauta, Mulungu wanu, akulola zimenezo kuti akuyeseni, kuti aone ngati mumamkondadi ndi mtima wanu wonse.
4Mutsate Chauta, Mulungu wanu, ndi kuwopa Iye yekha. Mutsate malamulo ake ndi kumvera mau ake. Mutumikire Iye ndi kuphathana naye.
5Koma aphedwe mneneri aliyense kapena womasulira maloto aliyense amene akuuzani kuti muukire Chauta, Mulungu wanu, amene adakutulutsani ku Ejipito ndi kukuwombolani m'dziko laukapolo. Munthu wotero ndi woipa, chifukwa akufuna kukusiyitsani njira imene Chauta akufuna kuti muitsate. Aphedwe, ndipo pakutero mudzachotsa choipa chimenechi pakati panu.
6Munthu atha kukunyengererani mobisa kuti mupembedze milungu ina, milungu imene inu ndi makolo anu simudaipembedzepo. Munthuyo ngakhale akhale mbale wanu weniweni wa mimba imodzi kapena mwana wanu wamwamuna kapena mwana wanu wamkazi, kapena mkazi wanu wokondedwa, kapena bwenzi lanu lapamtima, musaipembedze milunguyo mpang'ono pomwe.
7Milungu yake mwina idzakhala milungu ya anthu omwe mwayandikana nawo, kapena milungu ya amene mwatalikirana nawo.
8Inu musakopeke kapena kumvera zimene iyeyo akunena. Musamchitire chifundo kapena chisoni, ndipo musamtchinjirize.
9Mupheni! Yambani ndinu kumponya miyala, ndipo mutatero, pamenepo aliyense amponyenso miyala.
10Mumuphe ndi miyala. Iye adati akusokeretseni, kuti musiyane ndi Mulungu wanu amene adakutulutsani ku dziko la Ejipito kumene mudaali kuukapolo kuja.
11Tsono Aisraele onse adzamva zimene zachitikazo nadzachita mantha, ndipo palibe wina pakati panu amene adzachitenso choipa choterechi.
12Pomakhala m'midzi imene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsaniyo, nthaŵi zina kapena mudzamva
13kuti anthu ena a mtundu wanu asokeretsa anthu m'mizinda yao yomwe. Akuŵapembedzetsa milungu imene inu simudaipembedzepo nkale lonse.
14Mbiri yoteroyo muifufuze bwino. Mukapeza kuti mbiriyo njoona, kuti chinthu choipa choterechi chidachitikadi,
15pompo muphe anthu onse amumzindamo pamodzi ndi zoŵeta zomwe. Muwononge mudzi umenewo kotheratu.
16Zinthu zonse za anthu a mu mzinda umenewo muzisonkhanitse pamodzi, ndipo muziwunjike pakati pa bwalo lalikulu la mzindawo. Tsono mutatero, muutenthe mzindawo pamodzi ndi zonse zam'menemo, kuti zikhale ngati nsembe yopsereza kwa Chauta, Mulungu wanu. Muusiye choncho kuti ukhale bwinja mpaka muyaya.
17Musagwireko kanthu kena kalikonse koyenera kuwonongedwa. Tsono Chauta adzaleka osakukwiyiraninso, adzakumverani chisoni ndipo adzakuchitirani chifundo, nadzakuchulukitsani monga adalonjezera makolo anu.
18Adzakuchitirani zimenezi mukamamvera mau a Chauta, Mulungu wanu, mukamatsata malamulo ake amene ndikukuuzani lero, ndipo mukamachita zolungama pamaso pa Chauta, Mulungu wanu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.