Rut. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Bowazi akwatira Rute.

1Nthaŵi yomweyo Bowazi adapita ku chipata cha mzinda nakakhala pansi, pa bwalo losonkhanirana. Tsono adangoona wachibale ankanena uja akufika. Apo Bowazi adati, “Bwenzi langa, tapatukira kuno, ukhale pansi apa.” Munthu uja adapatuka nakhala pansi.

2Adaitananso atsogoleri khumi amumzindamo naŵauza kuti, “Takhalani pansi apa.” Iwo adakhala pansi.

3Tsono adauza munthu wachibale uja kuti, “Naomi amene wabwerera kuchokera ku dziko la Mowabu, akugulitsa munda umene udaali wa malemu Elimeleki, wachibale wathu.

4Choncho ndinaganiza zokuuza zimenezi, kuti ugule mundawo pamaso pa anthu amene ali panoŵa, ndi pamaso pa atsogoleri a abale athu. Ngati ufuna kugula, ugule. Koma ngati sufuna, undiwuze kuti ndidziŵe, pakuti palibe wina woti augule koma iweyo, ndipo pambuyo pa iwe pali ine.” Munthuyo adati, “Ndigula munda umenewo.”

5Tsono Bowazi adamuuza kuti, “Tsiku limene udzagule mundawo kwa Naomi, udzatenganso Rute Mmowabu, mai wamasiye uja, kuti dzina la malemu aja lisungike pa choloŵa chao.”

6Apo wachibaleyo adati, “Sindingathe kugula mundawo kuti ukhale wanga, kuwopa kuti ndingaononge choloŵa changa. Mugule ndinu, ine sindingathe.”

7 Deut. 25.9 Masiku amenewo, munthu akamachita malonda kapena kusinthana kanthu ndi mnzake, zinkayenda motere: ankavula nsapato imodzi napatsa mnzakeyo. Imeneyi ndiyo inali njira yochitira umboni m'dziko la Israele.

8Choncho pamene wachibale uja adauza Bowazi kuti, “Gulani ndinu mundawo,” adavula nsapato yake napatsa Bowazi.

9Tsono Bowazi adauza atsogoleri ndi anthu onse aja kuti, “Nonsenu ndinu mboni lero, kuti ine ndagula kwa Naomi zonse zimene zidaali za malemu Elimeleki, ndiponso zonse za malemu Kiliyoni ndi za malemu Maloni.

10Deut. 25.5, 6 Ndatenganso Rute Mmowabu uja, mkazi wa malemu Maloni, kuti akhale mkazi wanga, kuti dzina la malemulo lisungike pa choloŵa chake, ndipo lisafafanizike pakati pa abale ake ndiponso m'mudzi mwake. Nonsenu ndinu mboni lero lino.”

11Gen. 29.31 Apo anthu onse amene anali pachipata paja, pamodzi ndi atsogoleri aja, adati, “Inde, ndife mboni. Mkazi amene akudzaloŵa m'nyumba mwakoyo, Chauta amsandutse wofanafana ndi Rakele ndi Leya, akazi amene adamanga banja la Israele pombalira ana ambiri. Ukhale munthu wosasoŵa kanthu mu mzinda wa Efurata, ndipo ukhale munthu wotchuka mu mzinda wa Betelehemu.

12Gen. 38.27-30 Ana ako amene Chauta adzakupatse mwa mai ameneyu, adzamange banja longa la Perezi, amene Tamara adabalira Yuda.”

Zidzukulu za Bowazi.

13Choncho Bowazi adakwatira Rute, ndipo Chauta adadalitsa Ruteyo, mwakuti adatenga pathupi nabala mwana wamwamuna.

14Tsono akazi adauza Naomi kuti, “Ngwodala Chauta amene sadakusiyeni nokha opanda wachibale. Mwanayo dzina lake litchuke mu Israele.

15Mwanayo adzakupatsani moyo watsopano ndipo adzakuchirikizani mu ukalamba wanu. Inde wakubalirani mwana mpongozi wanu amene amakukondani, amene wakuwonetsani kuti akupambana ana aamuna asanu ndi aŵiri.”

16Naomi adanyamula mwanayo namfukata ndipo adakhala mlezi wake.

17Akazi achinansi ake adalengeza kuti, “Mwana wabadwa kwa Naomi.” Ndipo adamutcha dzina loti Obedi. Iyeyu adakhala bambo wake wa Yese, bambo wa Davide.

18Tsono zidzukulu za Perezi ndi izi: Perezi adabereka Hezironi,

19Hezironi adabereka Ramu, Ramu adabereka Aminadabu.

20Aminadabu adabereka Nasoni, Nasoni adabereka Salimoni.

21Salimoni adabereka Bowazi, Bowazi adabereka Obedi.

22Obedi adabereka Yese ndipo Yese adabereka Davide.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help