1Ndikulirira Chauta mokweza,
ndikupemba kwa Chauta mofuula.
2Ndikupereka madandaulo anga kwa Iye,
ndikutchula mavuto anga pamaso pake.
3Pamene mtima wanga ufooka,
Inu mumadziŵa zoti ndichite.
Adani anditchera msampha
m'njira imene ndimayendamo.
4Ndikayang'ana ku dzanja lamanja,
palibe ndi mmodzi yemwe wosamalako za ine.
Kulibe koti ndithaŵire,
palibe munthu wondisamala.
5Ndimalirira Inu Chauta,
ndimati, “Inu ndinu kothaŵira kwanga,
ndinu zanga zonse m'dziko la amoyo.”
6Imvani kulira kwanga,
pakuti ndataya mtima.
Pulumutseni kwa ondizunza,
chifukwa andiposa mphamvu.
7Tulutseni m'ndende
kuti ndizitamanda dzina lanu.
Anthu anu adzandizungulira,
chifukwa Inu mwandichitira zabwino zambiri.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.