1Chauta adandiwuza kuti,
“Tsono iwe, uimbe nyimbo yamadandaulo,
kuimbira akalonga aŵiri aja a ku Yerusalemu.
Mau ake unene kuti:
2“ ‘Mai wako anali ngati mkango waukazi
pakati pa mikango yaimuna.
Ankagona pakati pa mikango yaimuna
akulera ana ake.
3Adalera mmodzi mwa ana ake,
ndipo mwanayo adasanduka mkango.
Udaphunzira kugwira nyama,
nuyamba kudya anthu.
4Tsono mitundu ya anthu idachenjezana za mkangowo,
ndipo tsiku lina udagwa m'mbuna yao.
Adaukoka ndi ngoŵe
kupita nawo ku dziko la Ejipito.
5Mai uja ataona
kuti mwana ankamukhulupirirayu wagwidwa,
adakuzanso wina mwa ana ake,
namsandutsa mkango wamphamvu.
6Unkayendayenda pakati pa mikango inzake,
pakuti unali mkango wokhwima.
Udaphunzira kugwira nyama,
nuyamba kudya anthu.
7Udagwetsa malinga ao,
ndipo udaononga mizinda yao.
Onse a m'dzikolo adachita mantha
chifukwa cha phokoso la kubangula kwake.
8Tsono mitundu ya anthu,
makamaka a m'maiko ozungulira,
adabwera kudzalimbana nawo.
Adautchera ukonde,
ndipo udagweradi m'mbuna yao.
9Adaukoka ndi ngoŵe
nauponya m'chitatanga.
Adapita nawo kwa mfumu ya ku Babiloni,
mfumuyo nkuuponya m'ndende.
Choncho liwu lake silidamvekenso
ku mapiri a ku Israele.
Mtengo wamphesa wouma10“ ‘Mai wako anali ngati mpesa m'munda wa mphesa
wobzalidwa m'mbali mwa madzi.
Udabereka bwino ndipo unali ndi nthambi zambiri,
chifukwa panali madzi ambiri.
11Unali ndi nthambi zolimba
zoyenera kupangira ndodo zaufumu.
Udatalika nusomphoka pakati pa zomera zina,
ndipo unkaoneka bwino
chifukwa cha kutalika kwake
ndi kuchuluka kwa nthambi zake.
12Koma adauzula mwaukali naugwetsa pansi.
Udauma ndi mphepo yakuvuma,
zipatso zake zidayoyoka,
thunthu lake lidauma,
mtengo wonse nkupserera ndi moto.
13Tsono adauwokanso ku chipululu
ku dziko louma, lopanda madzi.
14Ndipo moto udayaka mumtengomo,
nupsereza nthambi ndi zipatso zake.
Motero ulibenso nthambi yolimba
yoti nkupangira ndodo ya mfumu.’ ”
Imeneyi ndi nyimbo yachisoni, ndipo yasanduka nyimbo yapamaliro.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.