Rut. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Elimeleki apita ku Mowabu ndi banja lake.

1Nthaŵi ina, pamene aweruzi ankalamulira Israele, mudaagwa njala m'dzikomo. Tsono munthu wina wa ku Betelehemu m'dziko la Yuda, adapita ndi mkazi wake ndi ana ake aŵiri, kukakhala nao mwakanthaŵi ku dziko la Mowabu.

2Munthuyo anali Elimeleki, mkazi wake anali Naomi. Ana ake aŵiriwo anali Maloni ndi Kiliyoni. Onsewo anali Aefurati a ku Betelehemu m'dziko la Yuda, koma adapita ku Mowabu nakhala komweko.

3Tsono Elimeleki mwamuna wa Naomi adamwalira, ndipo Naomiyo adatsala ndi ana aŵiri aja.

4Iwoŵa adakwatira akazi achimowabu. Wina dzina lake anali Olipa, winayo anali Rute. Adakhala ku Mowabuko pafupi zaka khumi.

5Koma Maloni ndi Kiliyoni adamwalira, kotero kuti Naomi adataya ana ake aŵiri aja, pamodzi ndi mwamuna wake yemwe.

Naomi ndi Rute abwerera ku Betelehemu.

6Pamenepo mkaziyo ndi apongozi ake aŵiri aja adayamba kukonza ulendo wobwerera kwao kuchokera ku Mowabu, poti anali atamva ku Mowabuko kuti Chauta adadalitsa anthu ake ndi kuŵapatsa chakudya.

7Choncho adanyamuka, pamodzi ndi apongozi akewo, kuchoka kumene ankakhala kuja, nayamba ulendo wobwerera ku dziko la Yuda.

8Tsono Naomi adauza apongozi ake aŵiri aja kuti, “Pitani, aliyense abwerere kwa mai wake. Chauta akuchitireni zabwino, monga momwe mudachitira malemu aja ndi ine ndemwe.

9Chauta akuthandizeni kuti mupeze pokhala, ndipo aliyense mwa inu akwatiwe.” Pompo adaŵampsompsona. Koma iwo adayamba kulira mokweza,

10nauza Naomiyo kuti, “Iyai, ife tipita nao kwa anthu akwanu.”

11Koma Naomi adaŵauza kuti, “Pepani ana anga, bwererani kwanu. Chifukwa chiyani mukufuna kupita nao? Kodi mukuganiza kuti ndingathe kubala ana ena aamuna, kuti adzakhale amuna anu?

12Bwererani ana anga, muzipita kwanu, pakuti ndakalamba kwambiri, sindingathenso kukhala ndi mwamuna. Ngakhale ndikadanena kuti chikhulupiriro chilipobe, ngakhale ndikadakhala ndi mwamuna usiku uno, kuti ndibale ana aamuna,

13kodi tsono mukadatha kudikira mpaka akule? Kodi zimenezi zikadakuletsani kukwatiwa? Ai, ana anga, zotere zikadandiŵaŵa kwambiri chifukwa cha inu, poona kuti sindinu koma ndine amene Chauta adafuna kuti ndizunzike.”

14Pamenepo iwo aja adayambanso kulira mokweza. Olipa adampsompsona mpongozi wake ndi kumulaŵira, koma Rute adakangamira Naomiyo.

15Tsono Naomi adauza Rute kuti, “Ona, mbale wako wabwerera kwao ndi kwa milungu yake. Nawenso bwerera, umulondole mbale wakoyo.”

16Koma Rute adamuuza kuti, “Musandiwumirize kuti ndikusiyeni kapena kuti ndisakutsateni. Kumene mupite inuko, inenso ndipita komweko, ndipo kumene mukakhale inuko, inenso ndikakhala komweko. Abale anu adzakhala abale anga, ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.

17Kumene inu mukafere, inenso ndikafera komweko ndi kuikidwa komweko. Chauta andichite choipa chilichonse chingakule motani, ngati kanthu kena kalikonse katisiyanitse, kupatula imfa.”

18Naomi ataona kuti Rute watsimikiza kupita nao, sadanenenso kanthu.

19Choncho aŵiriwo adapitirira ulendo wao, mpaka adakafika ku Betelehemu. Akaziwo atafika ku Betelehemuko, anthu onse am'mudzimo adatekeseka chifukwa cha iwowo. Tsono akazi ena ankati, “Kodi ameneyu ndi Naomi?”

20Iyeyo adaŵauza kuti, “Musamanditchule Naomi, koma muzinditchula Mara, poti Mphambe wandizunza kwambiri.

21Ndidaapita ndili ndi zinthu zambiri, koma Chauta wandibweza ndili wopanda kanthu. Motero munditchulirenji Naomi pamene Mphambe wandisautsa ndi kundigwetsera mavuto oŵaŵa?”

22Umu ndi m'mene Naomi adabwerera kuchokera ku Mowabu pamodzi ndi Rute mpongozi wake wachimowabu uja. Ndipo adafika ku Betelehemu pa nthaŵi yoyamba kudula barele.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help