Mk. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yesu achiritsa munthu wopuwala dzanja(Mt. 12.9-14; Lk. 6.6-11)

1Yesu adakaloŵanso m'nyumba yamapemphero. M'menemo mudaali munthu wina wopuwala dzanja.

2Anthu ena ankafuna chifukwa choti akamnenezere Yesuyo, motero ankangomuyang'anitsitsa kuti aone ngati achiritse munthuyo pa tsiku la Sabata.

3Yesu adalamula munthuyo kuti, “Imirira, bwera kutsogolo kuno.”

4Tsono adafunsa anthuwo kuti, “Kodi pa tsiku la Sabata chololedwa nchiti? Kuchitira anthu zabwino, kapena kuŵachita zoipa? Kupulumutsa moyo wa munthu, kapena kuuwononga?” Anthuwo adangoti chete.

5Pamenepo Yesu mtima wake udamuŵaŵa, poona kuti anali anthu okanika chotero, ndipo adaŵayang'ana ndi mkwiyo. Tsono adalamula munthuyo kuti, “Tambalitsa dzanja lako.” Iye adalitambalitsa, ndipo dzanja lakelo lidakhalanso bwino.

6Pamenepo Afarisi aja adatuluka nakachita upo ndi anthu a m'chipani cha Herode, kuti apangane njira yophera Yesu.

Chikhamu cha anthu ku Nyanja ya Galileya

7Yesu pamodzi ndi ophunzira ake adachokapo napita ku Nyanja ya Galileya. Khamu lalikulu la anthu lidamtsatira.

8Anthu ake anali a ku Galileya, ena a ku Yudeya ndi ku Yerusalemu, ena a ku Idumeya, ndi kutsidya kwa Yordani, ndiponso kudera la ku Tiro ndi ku Sidoni. Onsewo adaafika kwa Iye, chifukwa anali atamva zimene Iye ankachita.

9

19ndiponso Yudasi Iskariote (amene pambuyo pake adapereka Yesu kwa adani ake.)

Za Yesu ndi Belezebulu(Mt. 12.22-32; Lk. 11.14-23; 12.10)

20Pambuyo pake Yesu adapita kwao, ndipo anthu ambiri adasonkhananso, kotero kuti Iye ndi ophunzira ake analibe ndi mpata womwe wodyera chakudya.

21Achibale ake atamva zimenezi, adabwera kuti adzamtenge, chifukwa ankati, “Wachita misala.”

22 Mt. 9.34; 10.25 Aphunzitsi ena a Malamulo, amene adaabwera kuchokera ku Yerusalemu, ankanena kuti, “Munthu ameneyu wagwidwa ndi Belezebulu.” Ankatinso, “Mphamvu zimene iyeyu amatulutsira mizimu yoipa nzochokera kwa mkulu wa mizimuyo.”

23Tsono Yesu adaitana anthu kuti adze pafupi, nanena mwafanizo kuti, “Kodi a mu ufumu wa Satana angathe bwanji kutulutsana okhaokha?

24Anthu a mu ufumu uliwonse akayamba kuukirana, ufumuwo sungalimbe.

25Ndipo anthu a m'banja limodzi akayamba kugaŵikana, banja lotere silingalimbe.

26Tsono ngati a mu ufumu wa Satana aukirana okhaokha nagaŵikana, Satanayo sangalimbe, ndiye kuti watha basi.

27“Wina sangathe kungoloŵa m'nyumba ya munthu wamphamvu nkumulanda katundu wake. Amayamba wammanga, kenaka ndiye kufunkha za m'nyumba mwakemo.

28“Ndithu ndikunenetsa kuti anthu angathe kukhululukidwa machimo onse, ngakhalenso zonena zao zonse zomunyoza Mulunguyo.

29Lk. 12.10Koma aliyense wonyoza Mzimu Woyera, sadzakhululukidwa konse. Tchimo lakelo limakhala mpaka muyaya.”

30Yesu adalankhula zimenezi poona kuti anthu aja ankanena kuti, “Wagwidwa ndi mzimu woipa.”

Amai ake ndi abale ake a Yesu(Mt. 12.46-50; Lk. 8.19-21)

31Amai ake ndi abale ake a Yesu adabwera kunyumbako. Adaima panja, natuma anthu kuti akamuitane.

32Anthu ambirimbiri adaakhala pansi pomzungulira. Ndiye iwo aja adamuuza kuti, “Amai anu ndi abale anu ali panjapa, akukufunani.”

33Koma Iye adati, “Amai anga! Abale anga! Otinso?”

34Apo adayang'ana anthu amene anali pomzungulira aja nati, “Inetu amai anga ndi abale anga ndi aŵa.

35Aliyense wochita zimene Mulungu akufuna, ameneyo ndiye mbale wanga ndi mlongo wanga ndi amai anga.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help