Mas. 11 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za kukhulupirira ChautaKwa Woimbitsa Nyimbo. Salmo la Davide.

1Ndimathaŵira kwa Chauta.

Nanga mungathe bwanji kundiwuza kuti,

“Thaŵira ku mapiri ngati mbalame.

2Taonani, anthu oipa akunga uta

ndipo akwinja muvi pa nsinga,

kuti alase anthu a mtima wolungama.

3Tsono ngati maziko aonongeka,

nanga wolungama angachite chiyani?”

4Koma Chauta ali m'Nyumba yake yoyera,

Chauta mpando wake waufumu uli kumwamba.

Maso ake amapenya anthu onse ndi kuŵayesa.

5Chauta amayesa anthu olungama namakondwera nawo,

mtima wake umadana ndi anthu oipa okonda zachiwawa.

6Iye adzaŵagwetsera makala

ndi miyala yamoto ngati mvula,

adzaŵalanga ndi mphepo yotentha monga kuŵayenera.

7Paja Chauta ndi wolungama,

amakonda ntchito zolungama,

ndipo anthu olungama adzaona nkhope yake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help