Mas. 140 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero lopempha chitetezoKwa Woimbitsa Nyimbo. Salmo la Davide.

1Pulumutseni, Inu Chauta, kwa anthu oipa.

Tchinjirizeni kwa anthu ankhanza.

2Iwo amalingalira mumtima mwao

kuti achite zoipa,

amautsa nkhondo nthaŵi zonse.

3 Aro. 3.13 Amanola lilime lao kuti likhale ngati la njoka,

m'kamwa mwao muli ululu wa mamba.

4Inu Chauta, tetezeni kwa anthu oipa,

tchinjirizeni kwa anthu andeu,

amene amaganiza zofuna kundigwetsa.

5Anthu odzikuza anditchera msampha mobisika,

atchera ukonde wa zingwe,

anditchera misampha m'mbali mwa njira.

6Ndimauza Chauta kuti,

“Inu ndinu Mulungu wanga,”

tcherani khutu kuti mumve liwu la kupemba kwanga,

Inu Chauta.

7Inu Chauta, Ambuye anga, Mpulumutsi wanga wamphamvu,

mwateteza moyo wanga pa tsiku lankhondo.

8Inu Chauta, musampatse munthu woipa zokhumba zake.

Musathandizire chiwembu chake.

9Adani anga ondizinga asandigonjetse.

Mau ao otemberera aŵabwerere.

10Makala amoto aŵagwere,

aponyedwe m'maenje ozama, asatulukemonso.

11Musalole kuti woononga mbiri ya mnzake

akhazikike m'dziko.

Choipa chimlondole munthu wankhanza mpaka kumuwononga.

12Ndimadziŵa kuti Inu Chauta mumateteza ozunzika,

mumaweruza mwachilungamo anthu osoŵa.

13Zoonadi, anthu ochita zabwino adzatamanda dzina lanu.

Anthu amenewo adzakhala pamaso panu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help