Miy. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ubwino wake wa nzeru

1Mwana wanga, uvomere mau anga,

ndi kusunga bwino malamulo anga.

2Uzitchera khutu ku nzeru,

uziikapo mtima pa kumvetsa zinthu.

3Ndikutitu upemphe mtima wozindikira zinthu,

ndi kupemba kuti ukhale womvetsa zinthu.

4Uziifunafuna nzeruyo ngati siliva,

ndi kumaiwunguza ngati chuma chobisika.

5Ukatero, udzamvetsa za kuwopa Chauta,

udzapeza nzeru za kudziŵa Mulungu.

6 Lun. 9.10; Mphu. 1.1 Paja Chauta ndiye amapatsa nzeru,

Iye ndiye kasupe wa kudziŵa zinthu ndi wa kumvetsa.

7Amasungira anthu olungama nzeru zenizeni,

ali ngati chishango choteteza oyenda mwaungwiro.

8Ndiye mlonda wa njira zolungama,

amatchinjiriza njira ya anthu ake oyera mtima.

9Motero udzamvetsa za ungwiro ndi chilungamo,

za kusakondera, ndi za njira iliyonse yabwino.

10Nzeru zidzaloŵa mumtima mwako,

kudziŵa zinthu kudzakusangalatsa.

11Kuganiziratu zam'tsogolo kudzakusunga,

kumvetsa zinthu kudzakuteteza.

12Nzeruyo idzakupulumutsa ku mayendedwe oipa,

idzakuteteza kwa amtherakuŵiri,

13amene amasiya njira zolungama,

namayenda m'njira zamdima.

14Iwoŵa amakondwa pochita zoipa,

amasangalala ndi ntchito zosalungama.

15Anthu ameneŵa njira zao nzokhotakhota,

makhalidwe ao ngonyenga.

16Udzapulumuka kwa mkazi wadama,

kwa mkazi wachiwerewere wolankhula mau oshashalika,

17amene amasiya mwamuna wake wapaumbeta,

kuiŵala chipangano chochita ndi Mulungu wake.

18Pakuti nyumba yake imatsenderekera ku imfa,

njira zake zimamufikitsa kwa anthu akufa.

19Opita kwa iye, palibe ndi mmodzi yemwe wobwerako,

sazipezanso njira zopita ku moyo.

20Ndiye iwe, uzitsata njira za anthu abwino,

uziyenda m'njira za anthu ochita chilungamo.

21Paja anthu olungama ndiwo adzakhale m'dziko,

anthu okhulupirika ndiwo adzakhazikike m'menemo.

22Koma anthu oipa Mulungu adzaŵachotsa pa dziko,

anthu onyenga adzaŵatulutsa m'dzikomo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help