1 Yes. 65.17; Chiv. 20.11 Ndipo ndinaona m'mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m'mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka, ndipo kulibenso nyanja.
2Yes. 61.10; 2Ako. 11.2; Aheb. 11.10; 12.22; 13.14Ndipo ndinaona mzinda woyerawo, Yerusalemu watsopano, ulikutsika Kumwamba kwa Mulungu, wokonzeka ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wake.
3Ezk. 43.7Ndipo ndinamva mau aakulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao;
4Yes. 25.8; 35.10; 1Ako. 15.54ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.
52Ako. 5.17Ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu anati, Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano. Ndipo ananena, Talemba; pakuti mau awa ali okhulupirika ndi oona.
6Yes. 12.3; 54.11; Yoh. 4.10, 14; Chiv. 16.17Ndipo anati kwa ine, Zatha. Ine ndine Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza. Kwa iye wakumva ludzu ndidzampatsa amwe kukasupe wa madzi a moyo kwaulere.
7Aheb. 8.10Iye wakupambana adzalandira izi; ndipo ndidzakhala Mulungu wake, ndi iye adzakhala mwana wanga.
81Ako. 6.9-10; Chiv. 20.14-15Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.
Yerusalemu watsopano9 Chiv. 15.1, 6-7; 19.7 Ndipo anadza mmodzi wa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, zodzala ndi miliri yotsiriza isanu ndi iwiri; ndipo analankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa.
10Chiv. 21.2Ndipo ananditenga mu Mzimu kunka kuphiri lalikulu ndi lalitali, nandionetsa mzinda wopatulikawo, Yerusalemu, wotsika mu Mwamba kuchokera kwa Mulungu,
11ndipo unakhala nao ulemerero wa Mulungu; kuunika kwake kunafanana ndi mwala wa mtengo wake woposa, ngati mwala wayaspi, wonyezimira, ngati krustalo;
12Ezk. 48.31-34nukhala nalo linga lalikulu ndi lalitali, nukhala nazo zipata khumi ndi ziwiri, ndi pazipata angelo khumi ndi awiri, ndi maina olembedwapo, ndiwo maina a mafuko khumi ndi awiri a ana a Israele;
13kum'mawa zipata zitatu, ndi kumpoto zipata zitatu, ndi kumwera zipata zitatu, ndi kumadzulo zipata zitatu.
14Mat. 16.18Ndipo linga la mzinda linakhala nao maziko khumi ndi awiri, ndi pomwepo maina khumi ndi awiri a atumwi khumi ndi awiri a Mwanawankhosa.
15Ezk. 40.3Ndipo iye wakulankhula ndi ine anali nao muyeso, bango lagolide, kuti akayese mzindawo, ndi zipata zake, ndi linga lake.
16Ndipo mzinda ukhala waphwamphwa; utali wake ulingana ndi kupingasa kwake: ndipo anayesa mzinda ndi bangolo, mastadiya zikwi khumi ndi ziwiri; utali wake, ndi kupingasa kwake, ndi kutalika kwake zilingana.
17Ndipo anayesa linga lake, mikono zana mphambu makumi anai kudza zinai, muyeso wa munthu, ndiye mngelo.
18Ndipo mirimo ya linga lake ndi yaspi; ndipo mzindawo ngwa golide woyengeka, wofanana ndi mandala oyera.
19Yes. 54.11Maziko a linga la mzinda anakometsedwa ndi miyala ya mtengo, ya mitundumitundu; maziko oyamba, ndi yaspi; achiwiri, ndi safiro; achitatu, ndi kalikedo; achinai, ndi smaragido;
20achisanu, ndi sardonu; achisanu ndi chimodzi, ndi sardiyo; achisanu ndi chiwiri, ndi krusolito; achisanu ndi chitatu, ndi berulo; achisanu ndi chinai, ndi topaziyo; akhumi, ndi krusoprazo; akhumi ndi achimodzi, ndi huakinto; akhumi ndi chiwiri, ndi ametusto.
21Chiv. 22.2Ndipo zitseko khumi ndi ziwiri ndizo ngale khumi ndi ziwiri; chitseko chilichonse pa chokha cha ngale imodzi. Ndipo khwalala la mzinda nla golide woyengeka, ngati mandala openyekera.
22Yoh. 4.23Ndipo sindinaone Kachisi momwemo; pakuti Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, ndi Mwanawankhosa ndiwo Kachisi wake.
23Yes. 60.19-20Ndipo pamzinda sipafunika dzuwa, kapena mwezi wakuuwalira; pakuti ulemerero wa Mulungu uunikira umenewu, ndipo nyali yake ndiye Mwanawankhosa.
24Yes. 60.3, 5, 11Ndipo amitundu adzayendayenda mwa kuunika kwake; ndi mafumu a dziko atenga ulemerero wao kulowa nao momwemo.
25Yes. 60.11; 60.20Ndipo pazipata zake sipatsekedwa konse usana, (pakuti sikudzakhala usiku komweko);
26Chiv. 21.24ndipo adzatenga ulemerero ndi ulemu wa amitundu nadzalowa nao momwemo;
27Yes. 35.8; Chiv. 13.8; 22.14-15ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kalikonse kosapatulidwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.