MASALIMO 123 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Pemphero la wonyozedwaNyimbo yokwerera.

1 Mas. 121.1; 11.4 Ndikweza maso anga kwa Inu,

kwa Inu wakukhala kumwamba.

2Taonani, monga maso a anyamata

ayang'anira dzanja la ambuye wao,

monga maso a adzakazi

ayang'anira dzanja la mbuye wao wamkazi:

Momwemo maso athu ayang'anira Yehova Mulungu wathu,

kufikira atichitira chifundo.

3Mutichitire chifundo, Yehova, mutichitire chifundo;

pakuti takhuta kwambiri ndi mnyozo.

4Moyo wathu wakhuta ndithu

ndi kuseka kwa iwo osasowa kanthu,

ndi mnyozo wa odzikuza.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help