1Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,
2Wobadwa ndi munthu iwe, ipha mwambi, nunene fanizo kwa nyumba ya Israele,
3Ezk. 17.12-21nuziti, Atero Ambuye Yehova, Chiombankhanga chachikulu ndi mapiko aakulu, ndi maphiphi aatali, odzala nthenga cha mathothomathotho, chinafika ku Lebanoni, nkutenga nsonga ya mkungudza,
4chinabudula nsonga yosomphoka ya nthambi zake zanthete, ndi kumuka nayo kudziko la malonda, chinaiika m'mzinda wa amalonda.
5Yes. 44.4Chinatengakonso mbeu ya m'dziko, ndi kuibzala m'nthaka yokoma, chinaiika panali madzi ambiri, chinaioka ngati mtengo wamsondodzi.
6Ndipo inaphuka, nikhala mpesa wotambalala waufupi msinkhu, nthambi zake zinapindikira momwe, ndi mizu yake pansi pake, nikhala mpesa, nuonetsa nthambi ndi kuphuka mphukira.
7Panalinso chiombankhanga china chachikulu, ndi mapiko aakulu, ndi nthenga zambiri; ndipo taona, mpesa uwu unachipindira mizu yake, nuchilunjikitsira zake, kuchokera pookedwa pake, kuti chiuthirire madzi.
8Unaokedwa mu nthaka yabwino kuli madzi ambiri, kuti uphuke nthambi, nubale zipatso, nukhale mpesa wabwino.
92Maf. 25.6-7Uziti, Atero Ambuye Yehova, Udzakondwa kodi? Sadzausula ndi kudula zipatso zake, kuti uume, kuti masamba ake onse ophuka aume, ngakhale palibe mphamvu yaikulu, kapena anthu ambiri akuuzula?
10Inde ungakhale waokedwa udzakondwa kodi? Sudzauma chiumire kodi pakuuomba mphepo ya kum'mawa? Udzauma pookedwa apo udaphuka.
11Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti.
12Ezk. 17.3; 2Maf. 24.11-16Uziti, tsono kwa nyumba ya mpandukoyi, Simudziwa kodi izi nchiyani? Uziti, Taonani mfumu ya ku Babiloni inadza ku Yerusalemu, nkutenga mfumu yake ndi akalonga ake, nkubwera nao kuli iye ku Babiloni;
132Maf. 24.17ndipo inatenga wa mbumba yachifumu, nkuchita naye pangano, nkumlumbiritsa, nkuchotsa amphamvu a m'dziko;
14kuti ufumuwo ukhale wopepuka, kuti usadzikweze, koma kuti pakusunga pangano lake ukhale.
152Maf. 24.20Koma anapandukira ndi kutuma mithenga yake ku Ejipito, kuti ampatse akavalo ndi anthu ambiri. Adzapindula kodi? Adzapulumuka wakuchita izi? Athyole pangano ndi kupulumuka kodi?
16Yer. 32.5Pali Ine, ati Ambuye Yehova, pamalo pokhala mfumu, imene idamchititsa ufumu, imene anapeputsa lumbiro lake, imene anathyola pangano lake, adzafa pamodzi ndi iye pakati pa Babiloni.
17Yer. 37.5-7; 52.4Ndipo Farao ndi nkhondo yake yaikulu, ndi khamu lake launyinji, sadzachita pamodzi naye kunkhondo, pakuunda mtumbira, ndi kumanga malinga, kulikha anthu ambiri.
18Pakuti anapepula lumbiro, ndi kuthyola pangano, angakhale anapereka dzanja lake; popeza anachita izi zonse sadzapulumuka.
19Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Pali Ine, lumbiro langa, analipepula, ndi pangano langa analithyola, ndidzawabweza pamutu pake.
20Ndidzamphimbanso ndi ukonde wanga, nadzakodwa iye mu msampha wanga; ndipo ndidzadza naye ku Babiloni, ndi kunena naye komweko mlandu wa kulakwa kwake anandilakwira nako.
21Ndipo othawa ake onse m'magulu ake onse adzagwa ndi lupanga, ndi otsala adzabalalitsidwa kumphepo zonse; ndipo mudzadziwa kuti Ine Yehova ndanena.
22 Yes. 11.1; 53.2; Zek. 3.8 Atero Ambuye Yehova, Ndidzatenganso nsonga ya mkungudza wautali ndi kuiika; ndidzabudula nsonga yosomphoka ya nthambi zake zanthete, ndi kuioka paphiri lalitali lothuvuka;
23Dan. 4.12paphiri lothuvuka la Israele ndidzaioka, ndipo idzaphuka nthambi ndi kubala zipatso, nidzakhala mkungudza wokoma, ndi m'munsi mwake mudzakhala mbalame zilizonse za mapiko aliwonse; mu mthunzi wa nthambi zake zidzabindikira.
24Ezk. 22.14; Luk. 1.52Ndipo mitengo yonse yakuthengo idzadziwa kuti Ine Yehova ndatsitsa mtengo wosomphoka, ndakuza mtengo waung'ono, ndaumitsa mtengo wauwisi, ndi kuphukitsa mtengo wouma; Ine Yehova ndanena ndi kuchichita.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.