1 1Tim. 4.1 Koma zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthawi zowawitsa.
2Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika,
3osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudierekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino,
4achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu;
52Ate. 3.6akukhala nao maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.
6Pakuti mwa iwo akhala akukwawira m'nyumba, nagwira akazi opusa, osenza akatundu a zoipa zao, otengedwa nazo zilakolako za mitundumitundu:
7ophunzira nthawi zonse, koma sangathe konse kufikira kuchizindikiritso cha choonadi.
8Eks. 7.11Ndipo monga momwe Yane ndi Yambere anatsutsana naye Mose, kotero iwonso atsutsana nacho choonadi; ndiwo anthu ovunditsitsa mtima, osatsimikizidwa pachikhulupiriro.
9Koma sadzapitirirapo; pakuti kupusa kwao kudzaonekeratu kwa onse, monganso kupusa kwa iwo aja.
Timoteo alimbike kutsata ziphunzitso zokoma, ndi kulalikira nthawi zonse10 Afi. 2.22 Koma iwe watsatatsata chiphunzitso changa, mayendedwe, chitsimikizo mtima, chikhulupiriro, kuleza mtima, chikondi, chipiriro,
11Mac. 13.50; 14.2, 5-6, 19; 2Ako. 1.10mazunzo, kumva zowawa; zotere zonga anandichitira mu Antiokeya, mu Ikonio, mu Listara, mazunzo otere onga ndawamva; ndipo m'zonsezi Ambuye anandilanditsa.
12Mat. 16.24; Mac. 14.22Ndipo onse akufuna kukhala opembedza m'moyo mwa Khristu Yesu, adzamva mazunzo.
132Tim. 2.16Koma anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.
142Tim. 1.13Koma ukhalebe iwe mu izi zimene waziphunzira, nutsimikizika mtima nazo, podziwa amene adakuphunzitsa;
15Yoh. 5.39; 2Tim. 1.5ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.
16Aro. 15.4; 2Pet. 1.20-21Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m'chilungamo:
171Tim. 6.11kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.