MIYAMBO 19 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1Wosauka woyenda mwangwiro

aposa wokhetsa milomo ndi wopusa.

2Kukhumba kosadziwa sikuli kwabwino;

ndipo wofulumira ndi mapazi ake amachimwa.

3Utsiru wa munthu ukhotetsa njira yake;

mtima wake udandaula pa Yehova.

4Chuma chionjezetsa mabwenzi ambiri;

koma mnzake wa waumphawi amleka.

5 Deut. 19.16-19 Mboni yonama sidzakhala yosalangidwa;

wolankhula mabodza sadzapulumuka.

6Ambiri adzapembedza waufulu;

ndipo yense ndi bwenzi la munthu wopatsa.

7 Mas. 38.11 Abale onse a wosauka amuda;

nanga mabwenzi ake kodi satanimphirana naye?

Awatsata ndi mau, koma kuli zii.

8Wolandira nzeru akonda moyo wake;

wosunga luntha adzapeza zabwino.

9 Miy. 19.5 Mboni yonama sidzapulumuka chilango;

wolankhula mabodza adzaonongeka.

10 Mlal. 10.6-7 Wopusa sayenera kukhala ndi zinthu zolongosoka;

nanga kapolo ayenera kulamulira akalonga kodi?

11 Yak. 1.19 Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo;

ulemerero wake uli wakuti akhululukire cholakwa.

12Mkwiyo wa mfumu ukunga kubangula kwa mkango;

koma kukoma mtima kwake kunga mame pamsipu.

13Mwana wopusa ndiye tsoka la atate wake;

ndipo makangano a mkazi ndiwo kudonthadonthabe.

14 2Ako. 12.14 Nyumba ndi chuma ndizo cholowa cha atate;

koma mkazi wanzeru achokera kwa Yehova.

15Ulesi ugonetsa tulo tofa nato;

ndipo moyo wamkhongono udzamva njala.

16 Luk. 10.28 Wosunga lamulo asunga moyo wake;

wonyalanyaza mayendedwe ake adzafa.

17 Mat. 10.42; 2Ako. 9.6-8; Aheb. 6.10 Wochitira waumphawi chifundo abwereka Yehova;

adzambwezera chokoma chakecho.

18Menya mwanako, chiyembekezero chilipo,

osafunitsa kumuononga.

19Munthu waukali alipire mwini;

pakuti ukampulumutsa udzateronso.

20Tamvera uphungu, nulandire mwambo,

kuti ukhale wanzeru pa chimaliziro chako.

21 Yes. 46.10; Mac. 5.39 Muli zolingalira zambiri m'mtima mwa munthu;

koma uphungu wa Yehova ndiwo udzaimika.

22Chotikondetsa munthu ndicho kukoma mtima kwake;

ndipo wosauka apambana munthu wonama.

23 1Tim. 4.8 Kuopa Yehova kupatsa moyo;

wokhala nako adzakhala wokhuta;

zoipa sizidzamgwera.

24Waulesi alonga dzanja lake m'mbale,

osalibwezanso kukamwa kwake.

25Menya wonyoza, ndipo achibwana adzachenjera;

nudzudzule wozindikira adzazindikira nzeru.

26Wolanda za atate, ndi wopirikitsa amai,

ndiye mwana wochititsa manyazi ndi wogwetsa nkhope.

27Ukangofuna, mwananga, kusochera kusiya mau akudziwitsa,

leka kumva mwambo.

28Mboni yopanda pake inyoza chiweruzo;

m'kamwa mwa amphulupulu mumeza zoipa.

29Akonzera onyoza chiweruzo,

ndi mikwingwirima pamsana pa opusa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help