1Ku mitsinje ya ku Babiloni,
kumeneko tinakhala pansi, inde tinalira,
pokumbukira Ziyoni.
2Pa msondodzi uli m'mwemo
tinapachika mazeze athu.
3Popeza pamenepo akutigwirawo anatifunsa nyimbo
ndipo akutizunza anafuna tisekere,
ndi kuti, Mutiimbire nyimbo imodzi ya ku Ziyoni.
4 Neh. 2.3 Tidati, Tidzaimba bwanji nyimbo ya Yehova
m'dziko lachilendo?
5Ndikakuiwalani, Yerusalemu,
dzanja lamanja langa liiwale luso lake.
6 Ezk. 3.26 Lilime langa limamatike kunsaya zanga,
ndikapanda kukumbukira inu;
ndikapanda kusankha Yerusalemu
koposa chimwemwe changa chopambana.
7 Yer. 49.7-10; Ezk. 25.12 Yehova, kumbukirani ana a Edomu
tsiku la Yerusalemu;
amene adati, Gamulani, gamulani,
kufikira maziko ake.
8 Yes. 13.1-22 Mwana wamkazi wa ku Babiloni,
iwe amene udzapasulidwa;
wodala iye amene adzakubwezera chilango
monga umo unatichitira ife.
9Wodala iye amene adzagwira makanda ako,
ndi kuwaphwanya pathanthwe.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.