AGALATIYA 4 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Uthenga Wabwino utimasula kuchilamulo

1Koma ndinena kuti, pokhala wolowa nyumba ali wakhanda, sasiyana ndi kapolo, angakhale ali mwini zonse;

2komatu ali wakumvera omsungira ndi adindo, kufikira nthawi yoikika kale ndi atate wake.

3Agal. 2.4Koteronso ife, pamene tinali akhanda, tinali akapolo akumvera miyambo ya dziko lapansi;

4Mat. 1.23; Mrk. 1.15koma pokwaniridwa nthawi, Mulungu anatuma Mwana wake, wobadwa ndi mkazi, wobadwa wakumvera lamulo,

5Mat. 20.28; Yoh. 1.12kuti akaombole iwo akumvera lamulo, kuti ife tikalandire umwana.

6Aro. 8.15Ndipo popeza muli ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake alowe m'mitima yathu, wofuula Abba! Atate!

7Aro. 8.16-17Kotero kuti sulinso kapolo, koma mwana; koma ngati mwana, wolowa nyumbanso mwa Mulungu.

8 Aef. 2.11-12 Komatu pajapo, posadziwa Mulungu inu, munachitira ukapolo iyo yosakhala milungu m'chibadwidwe chao;

9Akol. 2.20koma tsopano, podziwa Mulungu inu, koma makamaka podziwika ndi Mulungu, mubwereranso bwanji kutsata miyambo yofooka ndi yaumphawi, imene mufuna kubwerezanso kuichitira ukapolo?

10Musunga masiku, ndi miyezi, ndi nyengo, ndi zaka.

11Agal. 2.2Ndiopera inu, kuti kapena ndadzivutitsa ndi inu chabe.

12Abale, ndikupemphani, khalani monga ine, pakuti inenso ndili monga inu. Simunandichitire choipa ine;

131Ako. 2.3koma mudziwa kuti m'kufooka kwa thupi ndinakulalikirani Uthenga Wabwino poyamba:

14Mat. 10.40ndipo chija cha m'thupi langa chakukuyesani inu simunachipeputse, kapena sichinakunyansireni, komatu munandilandira ine monga mngelo wa Mulungu, monga Khristu Yesu mwini.

15Pamenepo thamo lanu lili kuti? Pakuti ndikuchitirani inu umboni, kuti, kukadatheka, mukadakolowola maso anu ndi kundipatsa ine.

16Agal. 2.5, 14Kotero kodi ndasanduka mdani wanu, pakukunenerani zoona?

17Achita changu pa inu koma si kokoma ai, komatu afuna kukutsekerezani inu kunja, kuti mukawachitire iwowa changu.

18Koma nkwabwino kuchita changu m'zabwino nthawi zonse, si pokhapokha pokhala nanu pamodzi ine.

191Ako. 4.15Tiana tanga, amene ndilikumvanso zowawa za kubala inu, kufikira Khristu aumbika mwa inu,

20koma mwenzi nditakhala nanu tsopano, ndi kusintha mau anga; chifukwa ndisinkhasinkha nanu.

Sara ndi Hagara atifanizira mapangano awiriwo

21Ndiuzeni, inu akufuna kukhala omvera lamulo, kodi simukumva chilamulo?

22Gen. 16.15; 21.2Pakuti palembedwa, kuti Abrahamu anali nao ana aamuna awiri, mmodzi wobadwa mwa mdzakazi, ndi mmodzi wobadwa mwa mfulu.

23Gen. 18.10, 14; Aro. 9.7-8Komatu uyo wa mdzakazi anabadwa monga mwa thupi; koma iye wa mfuluyo, anabadwa monga mwa lonjezano. Izo ndizo zophiphiritsa;

24Eks. 19.1-6pakuti akaziwa ali mapangano awiri, mmodzi wa kuphiri la Sinai, akubalira ukapolo, ndiye Hagara.

25Koma Hagara ndiye phiri la Sinai, mu Arabiya, nafanana ndi Yerusalemu wa tsopano; pakuti ali muukapolo pamodzi ndi ana ake.

26Aheb. 12.22Koma Yerusalemu wa kumwamba uli waufulu, ndiwo amai wathu.

27Yes. 54.1Pakuti kwalembedwa,

Kondwera, chumba iwe wosabala;

imba nthungululu, nufuule iwe wosamva kuwawa kwa kubala;

pakuti ana ake a iye ali mbeta achuluka

koposa ana a iye ali naye mwamuna.

28 Mac. 3.25 Koma ife, abale, monga Isaki, tili ana a lonjezano.

29Gen. 21.9Komatu monga pompaja iye wobadwa monga mwa thupi anazunza wobadwa monga mwa Mzimu, momwemonso tsopano.

30Gen. 21.10, 12; Yoh. 8.35Koma lembo linena chiyani? Taya kubwalo mdzakazi ndi mwana wake, pakuti sadzalowa nyumba mwana wa mdzakazi pamodzi ndi mwana wa mfulu.

31Yoh. 8.36Chifukwa chake, abale, sitili ana a mdzakazi, komatu a mfulu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help