1 Ezr. 1.11 Munachita zovomereza dziko lanu, Yehova;
munabweza ukapolo wa Yakobo.
2 Mas. 32.1 Munachotsa mphulupulu ya anthu anu,
munafotsera zolakwa zao zonse.
3Munabweza kuzaza kwanu konse;
munabwerera kumkwiyo wanu wotentha.
4Mutibweze, Mulungu wa chipulumutso chathu,
nimuletse udani wanu wa pa ife.
5 Mas. 74.1 Kodi mudzatikwiyira nthawi zonse?
Kodi mudzakhala chikwiyire mibadwomibadwo?
6 Hab. 3.2 Kodi simudzatipatsanso moyo,
kuti anthu anu akondwerere ndi Inu?
7Tionetseni chifundo chanu, Yehova,
tipatseni chipulumutso chanu.
8 Hab. 2.1; Zek. 9.10 Ndidzamva cholankhula Mulungu Yehova;
pakuti adzalankhula zamtendere ndi anthu ake,
ndi okondedwa ake;
koma asabwererenso kuchita zopusa.
9 Yes. 46.13 Indedi chipulumutso chake chili pafupi
ndi iwo akumuopa Iye;
kuti m'dziko mwathu mukhale ulemu.
10 Yes. 32.17 Chifundo ndi choonadi zakomanizana;
chilungamo ndi mtendere zapsompsonana.
11 Yes. 45.8 Choonadi chiphukira m'dziko;
ndi chilungamo chasuzumira chili m'mwamba.
12 Mas. 67.6 Inde Yehova adzapereka zokoma;
ndipo dziko lathu lidzapereka zipatso zake.
13 Mas. 89.14 Chilungamo chidzamtsogolera;
ndipo chidzamkonzera mapazi ake njira.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.