1Ndidandaulira tsono, poyambayamba, kuti achitike mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko, chifukwa cha anthu onse;
2Ezr. 6.10; Yer. 29.7chifukwa cha mafumu ndi onse akuchita ulamuliro; kuti m'moyo mwathu tikakhale odika mtima ndi achete m'kulemekeza Mulungu, ndi m'kulemekezeka monse.
3Pakuti ichi nchokoma ndi cholandirika pamaso pa Mulungu Mpulumutsi wathu;
4Yoh. 3.16-17amene afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.
5Aro. 3.29-30; Aheb. 8.6Pakuti pali Mulungu mmodzi, ndi Mtetezi mmodzi pakati pa Mulungu ndi anthu, ndiye munthu, Khristu Yesu,
6Mrk. 10.45amene anadzipereka yekha chiombolo m'malo mwa onse; umboni m'nyengo zake;
7Aef. 3.7umene anandiika ine mlaliki wake ndi mtumwi (ndinena zoona, wosanama ine), mphunzitsi wa amitundu m'chikhulupiriro ndi choonadi.
8 Mas. 134.2; Yes. 1.15; Mala. 1.11; Yoh. 4.21 Chifukwa chake ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera, opanda mkwiyo ndi makani.
Zoyenera akazi9 1Pet. 3.3-4 Momwemonso, akazi adziveke okha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso; osati ndi tsitsi lake loluka, ndi golide kapena ngale, kapena malaya a mtengo wake wapatali;
101Pet. 3.3-4komatu (umo mokomera akazi akuvomereza kulemekeza Mulungu), mwa ntchito zabwino.
11Mkazi aphunzire akhale wachete m'kumvera konse.
121Ako. 14.34; Aef. 5.24Koma sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna; komatu akhale chete.
13Pakuti Adamu anayamba kulengedwa, pamenepo Heva;
14Gen. 3.6ndipo Adamu sananyengedwe, koma mkaziyo ponyengedwa analowa m'kulakwa;
15koma adzapulumutsidwa mwa kubala mwana, ngati akhala m'chikhulupiriro ndi chikondi ndi chiyeretso pamodzi ndi chidziletso.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.