EZEKIELE 25 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Aneneratu za kulangidwa kwa Aamoni

1Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti,

2Ezk. 21.28Wobadwa ndi munthu iwe, Lozetsa nkhope yako kwa ana a Amoni, nuwanenere;

3Miy. 17.5; Ezk. 26.2nunene kwa ana a Amoni, Tamverani mau a Ambuye Yehova, Atero Ambuye Yehova, Popeza unati, Ha! Kunena malo anga opatulika; muja anadetsedwa ndi kunena dziko la Israele; muja linapasuka ndi kunena nyumba ya Yuda; muja adalowa kundende;

4chifukwa chake taona, ndidzakupereka kwa ana a kum'mawa ukhale waowao, kuti amange misasa yao mwa iwe, namange pokhala pao mwa iwe, iwo adzadya zipatso zako ndi kumwa mkaka wako.

5Ezk. 21.20Ndipo ndidzayesa Raba khola la ngamira, ndi ana a Amoni popumula zoweta zazing'ono; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

6Zef. 2.8, 10, 15Pakuti atero Ambuye Yehova, Waomba manja, ndi kuvina, ndi kukondwera ndi chipeputso chonse cha moyo wako, kupeputsa dziko la Israele,

7chifukwa chake taona, ndakutambasulira dzanja langa, ndipo ndidzakupereka ukhale chofunkha cha amitundu, ndi kukudula mwa mitundu ya anthu, ndi kukutayikitsa m'maiko, ndidzakuononga; motero udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Za kulangidwa kwa Mowabu

8 Yes. 15—16 Atero Ambuye Yehova, Popeza Mowabu ndi Seiri akuti, Taona nyumba ya Yuda ikunga amitundu onse;

9chifukwa chake taona ndidzatsegula pambali pake pa Mowabu kuyambira kumizinda, kumizinda yake yokhala mphepete, yokometsetsa ya m'dziko, Beteyesimoti, Baala-Meoni, ndi Kiriyataimu,

10Ezk. 25.4kuwapereka kwa ana a kum'mawa pamodzi ndi ana a Amoni; ndipo ndidzawapereka akhale aoao, kuti ana a Amoni asakumbukikenso mwa amitundu;

11ndipo ndidzakwaniritsa maweruzo mu Mowabu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Za kulangidwa kwa Edomu

12 2Mbi. 28.17 Atero Ambuye Yehova, Popeza Edomu anachita mobwezera chilango pa nyumba ya Yuda, napalamula kwakukulu pakuibwezera chilango,

13chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ndidzatambasulira Edomu dzanja langa, ndi kulilikhira munthu ndi nyama, ndi kulisandutsa labwinja; kuyambira ku Temani mpaka Dedani adzagwa ndi lupanga.

14Amo. 9.12; Oba. 18Ndipo ndidzalibwezera Edomu chilango mwa dzanja la anthu anga Israele; ndipo adzachita mu Edomu monga mwa mkwiyo wanga, ndi ukali wanga; motero adzadziwa kubwezera chilango kwanga, ati Ambuye Yehova.

Za kulangidwa kwa Afilisti

15 2Mbi. 28.18 Atero Ambuye Yehova, Popeza Afilisti anachita mobwezera chilango nabwezera chilango ndi mtima wopeputsa kuononga, ndi udani wosatha,

16Zef. 2.4-5chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona ndidzatambasulira Afilisti dzanja langa, ndi kulikha Akereti, ndi kuononga otsalira mphepete mwa nyanja.

17Mas. 9.16Ndipo ndidzawabwezera chilango chachikulu, ndi malango ankharwe; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuwabwezera chilango Ine.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help