MIYAMBO 25 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Miyambo ya Solomoni yosonkhanitsa nthawi ya Hezekiya

1 1Maf. 4.32 Iyinso ndiyo miyambo ya Solomoni

imene anthu a Hezekiya mfumu ya Yuda anailemba.

2 Deut. 29.29; Aro. 11.33 Kubisa kanthu ndi ulemerero wa Mulungu;

koma ulemerero wa mafumu ndi kusanthula kanthu.

3Pamlengalenga patalika, ndi padziko pakuya,

koma mitima ya mafumu singasanthulike.

4 2Tim. 2.21 Chotsera siliva mphala yake,

mmisiri wa ng'anjo atulutsamo mbale.

5Chotsera woipa pamaso pa mfumu,

mpando wake udzakhazikika m'chilungamo.

6Usadzitame pamaso pa mfumu,

ngakhale kuima m'malo mwa akulu.

7 Luk. 14.8-10 Pakuti kunena kwa iwe, Takwera kuno,

kupambana ndi kuti utsitsidwe pamaso pa kalonga,

amene maso ako anamuona.

8 Mat. 5.25 Usatuluke mwansontho kukalimbana,

ungalephere pa kutha kwake,

atakuchititsa mnzako manyazi.

9Nena mlandu wako ndi mnzako,

osawulula zinsinsi za mwini;

10kuti wakumva angakutonze,

mbiri yako yoipa ndi kusachoka.

11 Yes. 50.4 Mau oyenera a pa nthawi yake

akunga zipatso zagolide m'nsengwa zasiliva.

12Monga mphete yagolide ndi chipini chagolide woyengeka,

momwemo wanzeru wodzudzula pa khutu lomvera.

13Monga chisanu cha chipale chofewa pa nthawi ya masika,

momwemo mthenga wokhulupirika kwa amene anamtuma;

atsitsimutsa moyo wa ambuyake.

14 Yud. 12 Monga mitambo ndi mphepo popanda mvula,

momwemo ndiye wodzikweza ndi zipatso zake monyenga.

15 Gen. 32.4-5 Chipiriro chipembedza mkulu;

lilime lofatsa lithyola fupa.

16Wapeza uchi kodi? Idyapo wokwanira,

kuti ungakukole, nusanze.

17Phazi lako lilowe m'nyumba ya mnzako kamodzikamodzi;

kuti angatope nawe ndi kukuda.

18 Mas. 57.4 Wochitira mnzake umboni wonama

ndiye chibonga, ndi lupanga, ndi muvi wakuthwa.

19Kukhulupirira munthu wa chiwembu tsiku latsoka

kunga dzino lothyoka ndi phazi loguluka.

20 Aro. 12.15 Monga wovula malaya tsiku lamphepo,

ngakhale kuthira vinyo wosasa m'soda,

momwemo woimbira nyimbo munthu wachisoni.

21 Mat. 5.44; Aro. 12.20 Mdani wako akamva njala umdyetse,

akamva ludzu ummwetse madzi.

22Pakuti udzaunjika makala amoto pamutu pake;

ndipo Yehova adzakupatsa mphotho.

23Mphepo ya kumpoto ifikitsa mvula;

chomwecho lilime losinjirira likwiyitsa nkhope.

24 Miy. 19.13 Kukhala pangodya ya tsindwi kufunika

kuposa kukhala m'nyumba ndi mkazi wolongolola.

25Monga madzi ozizira kwa munthu wotopa,

momwemo mau abwino akuchokera kudziko lakutali.

26Monga kasupe wopondedwa, ndi chitsime choonongeka,

momwemo wolungama ngati agonjera woipa.

27Kudya uchi wambiri sikuli kwabwino;

chomwecho kufunafuna ulemu wakowako sikuli ulemu.

28 Miy. 16.32 Wosalamulira mtima wake

akunga mzinda wopasuka wopanda linga.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help