1Ananu, mverani mwambo wa atate,
nimutchere makutu mukadziwe luntha;
2pakuti ndikuphunzitsani zabwino;
musasiye chilangizo changa.
3 1Mbi. 29.1 Pakuti ndinali mwana kwa atate wanga,
wokondedwa ndi mai, ndine ndekha, sanabale wina.
4Atate nandiphunzitsa, nati kwa ine,
mtima wako uumirire mau anga;
sunga malamulo anga, nukhale ndi moyo.
5Tenga nzeru, tenga luntha;
usaiwale, usapatuke pa mau a m'kamwa mwanga;
6usasiye nzeru, ndipo idzakusunga;
uikonde, idzakutchinjiriza.
7Nzeru ipambana, tatenga nzeru;
m'kutenga kwako konseko utenge luntha.
8Uilemekeze, ndipo idzakukweza;
idzakutengera ulemu pamene uifungatira.
9Idzaika chisada cha chisomo pamutu pako;
idzakupatsa korona wokongola.
10Tamvera mwananga, nulandire mau anga;
ndipo zaka za moyo wako zidzachuluka.
11Ndakuphunzitsa m'njira ya nzeru,
ndakuyendetsa m'mayendedwe olungama.
12Mapazi ako sadzaombana ulikuyenda;
ukathamanga, sudzaphunthwa.
13Gwira mwambo, osauleka;
uusunge; pakuti ndiwo moyo wako.
14 Mas. 1.1 Usalowe m'mayendedwe ochimwa,
usayende m'njira ya oipa.
15Pewapo, osapitamo;
patukapo, nupitirire.
16 Yes. 57.20 Pakuti akapanda kuchita zoipa, samagona;
ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tao tiwachokera.
17Pakuti amadya chakudya cha uchimo,
namwa vinyo wa chifwamba.
18 2Sam. 23.2, 4; Mat. 5.14-16 Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha,
kunkabe kuwala kufikira usana woti mbee.
19 1Sam. 2.9 Njira ya oipa ikunga mdima;
sadziwa chimene chiwaphunthwitsa.
20Mwananga, tamvera mau anga;
tcherera makutu ku zonena zanga.
21Asachoke kumaso ako;
uwasunge m'kati mwa mtima wako.
22 Deut. 32.46-47 Pakuti ali moyo kwa omwe awapeza,
nalamitsa thupi lao lonse.
23Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga;
pakuti magwero a moyo atulukamo.
24Tasiya m'kamwa mokhota,
uike patali milomo yopotoka.
25Maso ako ayang'ane m'tsogolo,
zikope zako zipenye moongoka.
26Sinkhasinkha bwino mayendedwe a mapazi ako;
njira zako zonse zikonzeke.
27 Yos. 1.7 Usapatuke kudzanja lamanja kapena kulamanzere;
suntha phazi lako kusiya zoipa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.