MIYAMBO 29 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1 1Sam. 2.25 Yemwe aumitsa khosi atadzudzulidwa kwambiri,

adzasweka modzidzimuka, palibe chomchiritsa.

2 Est. 3.15; 8.15 Pochuluka olungama anthu akondwa;

koma polamulira woipa anthu ausa moyo.

3 Luk. 15.13, 30 Mwamuna wokonda nzeru akondweretsa atate wake;

koma wotsagana ndi akazi adama amwaza chuma.

4Mfumu akhazikitsa dziko ndi chiweruzo;

koma wosonkhetsa anthu mphatso alipululutsa.

5Wosyasyalika mnzake

atcherera mapazi ake ukonde.

6M'kulakwa kwa woipa muli msampha;

koma wolungama aimba, nakondwera.

7 Mas. 41.1 Wolungama asamalira mlandu wa osauka;

koma woipa alibe nzeru yakuudziwa.

8Anthu onyoza atentha mzinda;

koma anzeru alezetsa mkwiyo.

9Munthu wanzeru akatsutsana ndi munthu wopusa,

ngakhale akwiya, ngakhale aseka, palibe mtendere.

10 Gen. 4.5, 8 Anthu ankhanza ada wangwiro;

koma oongoka mtima asamalira moyo wake.

11 Ower. 16.17 Chitsiru chivumbulutsa mkwiyo wake wonse;

koma wanzeru auletsa nautontholetsa.

12Mkulu akamvera chinyengo,

atumiki ake onse ali oipa.

13 Mat. 5.45 Waumphawi ndi wotsendereza akumana;

Yehova apenyetsa maso a onse awiriwo.

14Mfumu yolamulira osauka mwantheradi,

mpando wake udzakhazikika kufikira nthawi zonse.

15Nthyole ndi chidzudzulo zipatsa nzeru;

koma mwana womlekerera achititsa amake manyazi.

16 Mas. 92.11 Pochuluka oipa zolakwa zichuluka;

koma olungama adzaona kugwa kwao.

17 Miy. 13.24 Langiza mwana wako, ndipo adzakupumitsa;

nadzasangalatsa moyo wako.

18 1Sam. 3.1; Amo. 8.11-12; Yoh. 13.17; Yak. 1.25 Popanda chivumbulutso anthu amasauka;

koma wosunga chilamulo adalitsika.

19Kapolo sangalangizidwe ndi mau,

pakuti azindikira koma osavomera.

20Kodi uona munthu wansontho m'mau ake?

Ngakhale chitsiru chidzachenjera, koma ameneyo ai.

21Yemwe alera kapolo wake mwa ufulu kuyambira ubwana wake,

pambuyo pake adzadziyesa mwana wobala.

22Mwamuna wamkwiyo aputa makangano;

waukali achuluka zolakwa.

23 Yes. 66.2; Mat. 23.12; Mac. 12.23; Yak. 4.6, 10 Kudzikuza kwa munthu kudzamchepetsa;

koma wokhala ndi mtima wodzichepetsa adzalemekezedwa.

24Woyenda ndi mbala ada moyo wakewake;

amva kulumbira, koma osawulula kanthu.

25 Gen. 12.12, 14 Kuopa anthu kutchera msampha;

koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka.

26Ambiri afunafuna chiyanjano cha mkulu;

koma chiweruzo cha munthu chichokera kwa Yehova.

27Munthu woipa anyansa olungama;

ndipo woongoka m'njira anyansa wochimwa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help