1 1Sam. 2.24-25 Mwana wanzeru amamvera mwambo wa atate;
koma wonyoza samvera chidzudzulo.
2Munthu adzadya zabwino ndi zipatso za m'kamwa mwake;
koma moyo wa achiwembu udzadya chiwawa.
3 Yak. 3.2 Wogwira pakamwa pake asunga moyo wake;
koma woyasamula milomo yake adzaonongeka.
4Moyo wa waulesi ukhumba osalandira kanthu;
koma moyo wa akhama udzalemera.
5Wolungama ada mau onama;
koma woipa anyansa, nadzichititsa manyazi.
6Chilungamo chitchinjiriza woongoka m'njira;
koma udyo ugwetsa wochimwa.
7Alipo wodziyesa wolemera, koma alibe kanthu;
alipo wodziyesa wosauka, koma ali ndi chuma chambiri.
8Chiombolo cha moyo wa munthu ndicho chuma chake;
koma wosauka samva chidzudzulo.
9Kuunika kwa olungama kukondwa;
koma nyali ya oipa idzazima.
10Kudzikuza kupikisanitsa;
koma omwe anauzidwa uphungu ali ndi nzeru.
11Chuma cholandiridwa mokangaza chidzachepa;
koma wokundika ndi dzanja adzaona zochuluka.
12Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima;
koma pakufika chifunirocho ndicho mtengo wa moyo.
13 2Mbi. 36.16 Wonyoza mau adziononga yekha;
koma woopa malangizo adzalandira mphotho.
14 2Sam. 22.6-7 Malamulo a wanzeru ndiwo kasupe wa moyo,
apatutsa kumisampha ya imfa.
15Nzeru yabwino ipatsa chisomo;
koma njira ya achiwembu ili makolokoto.
16Yense wochenjera amachita mwanzeru;
koma wopusa aonetsa utsiru.
17Mthenga wolakwa umagwa m'zoipa;
koma mtumiki wokhulupirika alamitsa.
18Wokana mwambo adzasauka nanyozedwa;
koma wolabadira chidzudzulo adzalemekezedwa.
19Chifuniro chikondweretsa moyo chitachitidwa;
koma kusiya zoipa kunyansa opusa.
20Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru:
koma mnzao wa opusa adzaphwetekedwa.
21 Mas. 32.10 Zoipa zilondola ochimwa;
koma olungama adzalandira mphotho yabwino.
22Wabwino asiyira zidzukulu zake cholowa chabwino;
koma wochimwa angosungira wolungama chuma chake.
23M'kulima kwa osauka muli zakudya zambiri;
koma zinazo zimaonongeka posowa chiweruzo.
24 Miy. 23.13 Wolekerera mwanake osammenya amuda;
koma womkonda amyambize kumlanga.
25 Mas. 34.10 Wolungama adya nakhutitsa moyo wake;
koma mimba ya oipa idzasowa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.