YESAYA 54 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Zokoma zimene Yehova adzachitira Mpingo wao

1 Agal. 4.27 Imba, iwe wouma, amene sunabale; imba zolimba ndi kufuula zolimba, iwe amene sunabale mwana; pakuti ana a mfedwa achuluka koposa ana a mkazi wokwatibwa ndi mwamuna, ati Yehova.

2Kuza malo a hema wako, afunyulule zinsalu za mokhalamo iwe; usaleke, tanimphitsa zingwe zako, limbitsa zikhomo zako.

3Yes. 61.9Pakuti iwe udzafalikira ponse padzanja lamanja ndi lamanzere, ndipo mbeu yako idzalandira amitundu cholowa chao, ndi kukhalitsa anthu m'mabwinja.

4Usaope, pakuti sudzakhala ndi manyazi; usasokonezedwe, pakuti sudzachitidwa manyazi; pakuti udzaiwala manyazi a ubwana wako, ndi chitonzo cha umasiye wako sudzachikumbukiranso.

5Yer. 3.14; Aro. 3.29Pakuti Mlengi wako ndiye mwamuna wako; Yehova wa makamu ndiye dzina lake; ndi Woyera wa Israele ndiye Mombolo wako; Iye adzatchedwa Mulungu wa dziko lonse lapansi.

6Pakuti Yehova wakuitana iwe monga mkazi wakusiyidwa ndi wosauka m'mzimu, ngakhale mkazi wa ubwana wochotsedwa, ati Mulungu wako.

7Yer. 31.3; 2Ako. 4.17Kamphindi kakang'ono ndakusiya iwe, koma ndi chifundo chambiri ndidzakusonkhanitsa.

8M'kukwiya kwa kusefukira ndinakubisira nkhope yanga kamphindi; koma ndi kukoma mtima kwa chikhalire ndidzakuchitira chifundo, ati Yehova Mombolo wako.

9Gen. 9.11Pakuti kumeneku kuli kwa Ine monga madzi a Nowa; pakuti monga ndinalumbira kuti madzi a Nowa sadzamizanso padziko lapansi, momwemo ndinalumbira kuti sindidzakukwiyira iwe, pena kukudzudzula.

10Mas. 46.1-2; Yes. 51.6; Mat. 5.18Pakuti mapiri adzachoka, ndi zitunda zidzasunthika; koma kukoma mtima kwanga sikudzakuchokera iwe, kapena kusunthika chipangano changa cha mtendere, ati Yehova amene wakuchitira iwe chifundo.

11Iwe wosautsidwa, wobelukabeluka ndi namondwe, wosatonthola mtima, taona, ndidzakhazika miyala yako m'mawangamawanga abwino, ndi kukhazika maziko ako ndi masafiro.

12Ndipo ndidzamanga mazenera ako ndi miyala yofiira, ndi zipata zako ndi bareketi, ndi malire ako onse ndi miyala yokondweretsa.

13Yoh. 6.45; 1Ate. 4.9Ndipo ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.

14M'chilungamo iwe udzakhazikitsidwa, udzakhala kutali ndi chipsinjo, pakuti sudzaopa; udzakhala kutali ndi mantha, pakuti sadzafika chifupi ndi iwe.

15Taona, iwo angasonkhanitse pamodzi, koma si ndi Ine; aliyense amene adzasonkhana pamodzi akangane ndi iwe adzagwa chifukwa cha iwe.

16Taona, ndalenga wachipala amene avukuta moto wamakala, ndi kutulutsamo chida cha ntchito yake; ndipo ndalenga woononga kuti apasule.

17Yes. 45.24-25Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m'chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chao chimene chifuma kwa Ine, ati Yehova.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help