MASALIMO 106 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Israele anapikisana ndi Yehova kwambiri, Iye nawalanga nawalanditsanso. Amlemekezepo

1 Aleluya.

Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino:

Pakuti chifundo chake nchosatha.

2 Mas. 40.5 Adzafotokoza ndani ntchito zamphamvu za Yehova,

adzamveketsa ndani chilemekezo chake chonse?

3 Mac. 24.16; Agal. 6.9 Odala iwo amene asunga chiweruzo,

iye amene achita chilungamo nthawi zonse.

4Mundikumbukire, Yehova,

monga momwe muvomerezana ndi anthu anu;

mundionetsa chipulumutso chanu:

5Kuti ndione chokomacho cha osankhika anu,

kuti ndikondwere nacho chikondwerero cha anthu anu,

kuti ndidzitamandire pamodzi ndi cholowa chanu.

6 1Maf. 8.47 Talakwa pamodzi ndi makolo athu;

tachita mphulupulu, tachita choipa.

7 Eks. 14.11-12 Makolo athu sanadziwitse zodabwitsa zanu mu Ejipito;

sanakumbukire zachifundo zanu zaunyinji;

koma anapikisana ndi Inu kunyanja, ku Nyanja Yofiira.

8Koma anawapulumutsa chifukwa cha dzina lake,

kuti adziwitse chimphamvu chake.

9 Eks. 13.21 Ndipo anadzudzula Nyanja Yofiira, ndipo inaphwa:

Potero anawayendetsa mozama ngati m'chipululu.

10Ndipo anawapulumutsa m'dzanja la iye amene anawada,

nawaombola kudzanja la mdani.

11 Eks. 14.27 Ndipo madziwo anamiza owasautsa;

sanatsale mmodzi yense.

12 Eks. 15.1-21 Pamenepo anavomereza mau ake;

anaimbira chomlemekeza.

13 Eks. 15.24 Koma anaiwala ntchito zake msanga;

sanalindire uphungu wake:

14 Num. 11.4, 33; 1Ako. 10.6 Popeza analakalakatu kuchidikhako,

nayesa Mulungu m'chipululu.

15 Yes. 10.15-16 Ndipo anawapatsa chopempha iwo;

koma anaondetsa mitima yao.

16 Num. 16.1-35 Ndipo kumisasa anachita nao nsanje Mose

ndi Aroni woyerayo wa Yehova.

17Dziko lidayasama nilidameza Datani,

ndipo linafotsera gulu la Abiramu.

18Ndipo m'gulu mwao mudayaka moto;

lawi lake lidapsereza oipawo.

19 Eks. 32.4 Anapanga mwanawang'ombe ku Horebu,

nagwadira fano loyenga.

20 Aro. 1.23 M'mwemo anasintha ulemerero wao

ndi fanizo la ng'ombe yakudya msipu.

21Anaiwala Mulungu Mpulumutsi wao,

amene anachita zazikulu mu Ejipito;

22zodabwitsa m'dziko la Hamu,

zoopsa ku Nyanja Yofiira.

23 Eks. 32.10-11, 32 Potero Iye adati awaononge,

pakadapanda Mose wosankhika wake,

kuima pamaso pake pogamukapo,

kubweza ukali wake ungawaononge.

24 Num. 14.2-4 Anapeputsanso dziko lofunika,

osavomereza mau ake;

25koma anadandaula m'mahema mwao,

osamvera mau a Yehova.

26 Num. 14.29-30 Potero anawasamulira dzanja lake,

kuti awagwetse m'chipululu:

27Kugwetsanso mbeu zao mwa amitundu,

ndi kuwabalalitsa m'maiko maiko.

28 Num. 23.25 Ndipo anadziphatikiza ndi Baala-Peori,

nadyanso nsembe za akufa.

29Ndipo anamkwiyitsa nazo zochita zao;

kotero kuti mliri unawagwera.

30 Num. 25.7-13 Pamenepo panauka Finehasi, nachita chilango:

Ndi mliriwo unaletseka.

31Ndipo adamuyesa iye wachilungamo,

ku mibadwomibadwo kunthawi zonse.

32 Num. 20.2-13 Anautsanso mkwiyo wake kumadzi a Meriba,

ndipo kudaipira Mose chifukwa cha iwowa:

33Pakuti anawawitsa mzimu wake,

ndipo analankhula zosayenera ndi milomo yake.

34 Ower. 1.1-2, 27-36 Sanaononga mitunduyo ya anthu,

imene Yehova adawauza;

35koma anasokonekerana nao amitundu,

naphunzira ntchito zao:

36 Ower. 2.12-13, 17 Ndipo anatumikira mafano ao,

amene anawakhalira msampha:

37 2Maf. 16.3 Ndipo anapereka ana ao aamuna ndi aakazi nsembe ya kwa ziwanda,

38nakhetsa mwazi wosachimwa,

ndiwo mwazi wa ana ao aamuna ndi aakazi,

amene anawaperekera nsembe mafano a Kanani;

m'mwemo analidetsa dziko ndi mwaziwo.

39Ndipo anadziipsa nazo ntchito zao,

nachita chigololo nao machitidwe ao.

40 Ower. 2.14-15 Potero udayaka mkwiyo wa Yehova pa anthu ake,

nanyansidwa Iye ndi cholowa chake.

41Ndipo anawapereka m'manja a amitundu;

ndipo odana nao anachita ufumu pa iwo.

42Adani ao anawasautsanso,

nawagonjetsa agwire mwendo wao.

43 Ower. 2.16, 18 Iye anawalanditsa kawirikawiri;

koma anapikisana ndi Iye mwa uphungu wao,

ndi mphulupulu zao zinawafoketsa.

44Koma anapenya nsautso yao,

pakumva kufuula kwao:

45 Lev. 26.41-42 Ndipo anawakumbukira chipangano chake,

naleza monga mwa kuchuluka kwa chifundo chake.

46 Ezr. 9.9 Ndipo anawachitira kuti apeze nsoni

pamaso pa onse amene adawamanga ndende.

47 1Mbi. 16.35-36 Tipulumutseni, Yehova, Mulungu wathu,

ndi kutisokolotsa kwa amitundu,

kuti tiyamike dzina lanu loyera,

ndi kudzitamandira nacho chilemekezo chanu.

48Wodala Yehova, Mulungu wa Israele,

kuyambira kosayamba kufikira kosatha.

Ndi anthu onse anene, Amen.

Aleluya.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help