1Ndipo mfumu Solomoni anali mfumu ya Israele yense.
2Ndipo akulu a mfumu ndi awa: Azariya mwana wa Zadoki anali wansembe,
32Sam. 20.24Elihorefe ndi Ahiya ana a Sisa alembi, Yehosafati mwana wa Ahiludi wolembera mbiri,
4ndi Benaya mwana wa Yehoyada anali kazembe wa nkhondo, ndi Zadoki ndi Abiyatara anali ansembe,
5ndi Azariya mwana wa Natani anayang'anira akapitao, ndipo Zabudi mwana wa Natani anali wansembe ndi nduna yopangira mfumu,
6ndi Ahisara anayang'anira banja la mfumu, ndi Adoniramu mwana wa Abida anali wamsonkho.
7Ndipo Solomoni anali nao akapitao khumi ndi awiri akuyang'anira Aisraele onse, akufikitsira mfumu ndi banja lake zakudya; aliyense anafikitsa zakudya zofikira mwezi umodzi wa chaka.
8Ndipo maina ao ndiwo: Benihuri anatengetsa ku mapiri a Efuremu;
9Benedekere ku Makazi ndi Saalibimu ndi Betesemesi ndi Elonibetehanani;
10Benihesedi ku Aruboti ndi Soko ndi dziko lonse la Hefere;
11Benabinadabu ku mtunda wa Dori, mkazi wake ndiye Tafati mwana wa Solomoni;
12Baana mwana wa Ahiludi ku Taanaki ndi Megido ndi Beteseani konse, ali pafupi ndi Zaretani kunsi kwa Yezireele, kuyambira ku Beteseani kufikira ku Abele-Mehola, kufikiranso kundunji ku Yokomeamu;
13Benigebere ku Ramoti Giliyadi, iyeyo anali nayo mizinda ya Yairi mwana wa Manase ili mu Giliyadiyo, iye anali nalo dziko la Arigobu lili mu Basani, mizinda yaikulu makumi asanu ndi limodzi yamalinga ndi zitseko zamkuwa;
14Abinadabu mwana wa Ido ku Mahanaimu;
15Ahimaazi ku Nafutali, iyeyu adakwatira Basemati mwana wa Solomoni;
16Baana mwana wa Husai ku Asere ndi ku Bealoti;
17Yehosafati mwana wa Paruwa ku Isakara;
18Simei mwana wa Ela ku Benjamini;
19Deut. 3.8Gebere mwana wa Uri ku dziko la Giliyadi, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi la Ogi mfumu ya Basani; munalibe kapitao wina m'deramo.
201Maf. 3.8Ayuda ndi Aisraele anachuluka ngati mchenga wa kunyanja, namadya namamwa namakondwera.
21 Gen. 15.18; Mas. 72.10-11 Ndipo Solomoni analamulira maiko onse, kuyambira ku Yufurate kufikira ku dziko la Afilisti ndi ku malire a Ejipito; anthu anabwera nayo mitulo namtumikira Solomoni masiku onse a moyo wake.
22Ndipo zakudya za Solomoni zofikira tsiku limodzi zinali miyeso makumi atatu ya ufa wosalala, ndi miyeso makumi asanu ndi limodzi ya ufa wamankhupete,
23ng'ombe zonenepa khumi, ndi ng'ombe za kubusa makumi awiri, ndi nkhosa zana limodzi, osawerenganso ngondo ndi nswala ndi mphoyo ndi mbalame zoweta.
241Mbi. 22.9Pakuti analamulira dziko lonse lili tsidya lino la Yufurate, kuyambira ku Tifisa kufikira ku Gaza, inde mafumu onse a ku tsidya lino la Yufurate; nakhala ndi mtendere kozungulira konseko.
25Mik. 4.4Ndipo Ayuda ndi Aisraele anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake, kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, masiku onse a Solomoni.
26Ndipo Solomoni anali nazo zipinda za akavalo a magaleta ake zikwi khumi mphambu ziwiri.
27Ndipo akapitao aja anatengetsera chakudya Solomoni ndi anthu onse akudya ku gome la mfumu Solomoni, munthu yense m'mwezi mwake, sanalole kanthu kasoweke.
28Barelenso ndi udzu wa akavalo ndi ngamira anabwera nazo kumalo kwao, munthu yense monga momwe anamuuzira.
Nzeru ya Solomoni29 1Maf. 3.12 Ndipo Mulungu anampatsa Solomoni nzeru ndi luntha lambiri, ndi mtima wodziwa za mitundumitundu, zonga mchenga uli m'mphepete mwa nyanja.
30Mac. 7.22Ndipo nzeru ya Solomoni inaposa nzeru za anthu onse akum'mawa, ndi nzeru zonse za ku Ejipito.
311Maf. 4.29Pakuti anali wanzeru woposa anthu onse, woposa Etani wa ku Ezara, ndi Hemani, ndi Kalikoli, ndi Darida ana a Maholi; ndipo mbiri yake inafikira amitundu onse ozungulira.
32Miy. 1.1; Mlal. 1.1Ndipo ananena miyambo zikwi zitatu, ndipo nyimbo zake zinali chikwi chimodzi mphambu zisanu.
33Nakamba za mitengo, kuyambira mkungudza uli ku Lebanoni kufikira hisope wophuka pakhoma; anakambanso za nyama ndi mbalame ndi zinthu zokwawa pansi ndi za nsomba.
341Maf. 10.1; 2Mbi. 9.23Ndipo anafikapo anthu a mitundu yonse kudzamva nzeru ya Solomoni, ochokera kwa mafumu onse a dziko lonse lapansi, amene adamva mbiri ya nzeru yake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.