MIYAMBO 28 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Mau olinganiza zosiyana

1 Lev. 26.17, 36; Mas. 53.5 Woipa athawa palibe momthamangitsa;

koma olungama alimba mtima ngati mkango.

2Pochimwa dziko akalonga ake achuluka;

koma anthu ozindikira ndi odziwa

alikhazikikitsa nthawi yaikulu.

3 Mat. 18.28 Munthu waumphawi wotsendereza osauka

akunga mvula yamadzi yokokolola dzinthu.

4 Aro. 1.32 Omwe asiya chilamulo atama oipa;

koma omwe asunga chilamulo akangana nao.

5 Yoh. 7.17; 1Yoh. 2.20, 27 Oipa samvetsetsa chiweruzo;

koma omwe afuna Yehova amvetsetsa zonse.

6Waumphawi woyenda mwangwiro

apambana ndi yemwe akhotetsa njira zake, angakhale alemera.

7Wosunga chilamulo ndiye mwana wozindikira;

koma mnzao wa adyera achititsa atate wake manyazi.

8 Mlal. 2.26 Wochulukitsa chuma chake, pokongoletsa ndi phindu,

angokundikira yemwe achitira osauka chisoni.

9 Zek. 7.11-12; Mas. 109.7 Wopewetsa khutu lake kuti asamve chilamulo,

ngakhale pemphero lake linyansa.

10 Miy. 26.27 Wosocheretsa oongoka mtima alowe m'njira yoipa,

adzagwa mwini m'dzenje lake;

koma angwiro adzalandira cholowa chabwino.

11Wolemera adziyesa wanzeru;

koma wosauka wozindikira aululitsa zake.

12Posekera olungama pali ulemerero wambiri;

koma pouka oipa anthu amabisala.

13 Mas. 32.3, 5; 1Yoh. 1.8-10 Wobisa machimo ake sadzaona mwai;

koma wakuwavomereza, nawasiya adzachitidwa chifundo.

14 Mas. 16.8; Aro. 2.5 Wodala munthu wakuopa kosalekeza;

koma woumitsa mtima wake adzagwa m'zoipa.

15Monga mkango wobangula ndi chilombo choyendayenda,

momwemo mfumu yoipa ya anthu osauka.

16Kalonga wosowa nzeru apambana kusautsa;

koma yemwe ada chisiriro adzatanimphitsa moyo wake.

17Wopalamula mlandu wakupha munthu adzathawira kudzenje;

asamuletse.

18Woyenda mwangwiro adzapulumuka;

koma wokhota m'mayendedwe ake adzagwa posachedwa.

19 Miy. 12.11 Wolima munda wake zakudya zidzamkwanira;

koma wotsata anthu opanda pake umphawi udzamkwanira.

20 1Tim. 6.9 Munthu wokhulupirika ali ndi madalitso ambiri;

koma wokangaza kulemera sadzapulumuka chilango.

21 Miy. 24.23 Chetera silili labwino,

ngakhale kulakwa kuti ukadye kanthu.

22Mwini diso lankhwenzule akangaza kulemera,

osadziwa kuti umphawi udzamfikira.

23 Ezk. 13.19 Adzamkomera mtima wodzudzula m'tsogolo mwake,

koposa wosyasyalika ndi lilime lake.

24Wobera atate wake, pena amake, nati, Palibe kulakwa;

ndiye mnzake wa munthu wopasula.

25 1Tim. 6.6 Wodukidwa mtima aputa makangano;

koma wokhulupirira Yehova adzakula.

26Wokhulupirira mtima wakewake ali wopusa;

koma woyenda mwanzeru adzapulumuka.

27 Deut. 15.7-11 Wogawira aumphawi sadzasowa;

koma wophimba maso ake adzatembereredwa kwambiri.

28 Yob. 24.2-4 Pouka oipa anthu amabisala;

koma pakufa amenewo olungama achuluka.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help