YOSWA 20 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Mizinda yopulumukirako(Num. 35.9-34)

1Ndipo Yehova anati kwa Yoswa,

2Num. 35.11-14Nena ndi ana a Israele ndi kuti, Mudziikire mizinda yopulumukirako, monga ndinanena kwa inu mwa dzanja la Mose.

3Kuti athawireko wakupha munthu osamupha dala, osadziwa; ndipo idzakhalire inu yopulumukirako, kumpulumuka wolipsa mwazi.

4Deut. 21.19; Rut. 4.1-2Munthu akathawira umodzi wa mizinda iyi, aziima polowera pa chipata cha mzindawo, nafotokozere mlandu wake m'makutu a akulu a mzindawo; pamenepo azimlandira kumzinda kwao, ndi kumpatsa malo, kuti akhale pakati pao.

5Ndipo akamlondola wolipsa mwazi, asampereke m'dzanja lake wakupha mnzakeyo; pakuti anakantha mnansi wake mosadziwa, osamuda kale.

6Ndipo azikhala m'mzindamo mpaka adzaima pamaso pa msonkhano anene mlandu wake, mpaka atafa mkulu wa ansembe wa m'masiku omwewo; pamenepo wakupha mnzake azibwerera ndi kufika kumzinda kwake, ndi nyumba yake, kumzinda kumene adathawako.

7Yos. 21.13, 21, 32; 1Mbi. 6.76; 2Mbi. 10.1Ndipo anapatula Kedesi mu Galileya ku mapiri a Nafutali, ndi Sekemu ku mapiri a Efuremu, ndi mudzi wa Ariba ndiwo Hebroni ku mapiri a Yuda.

8Yos. 21.27, 36, 38Ndipo tsidya lija la Yordani kum'mawa kwa Yeriko, anaika Bezeri m'chipululu, kuchidikha, wa fuko la Rubeni, ndi Ramoti mu Giliyadi wa fuko la Gadi, ndi Golani mu Basani wa fuko la Manase.

9Num. 35.15Iyi ndi mizinda yoikidwira ana onse a Israele, ndi mlendo wakukhala pakati pao kuti athawireko aliyense wakupha munthu, ndi kuti asafe ndi dzanja la wolipsa mwazi, asanaime pamaso pa msonkhano.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help