1 Num. 6.25 Atichitire chifundo Mulungu, ndi kutidalitsa,
atiwalitsire nkhope yake;
2 Luk. 2.30, 41 kuti njira yanu idziwike padziko lapansi,
chipulumutso chanu mwa amitundu onse.
3Anthu akuyamikeni, Mulungu;
anthu onse akuyamikeni.
4 96.10, 13 Anthu akondwere, nafuule mokondwera;
pakuti mudzaweruza anthu molunjika,
ndipo mudzalangiza anthu padziko lapansi.
5Anthu akuyamikeni, Mulungu;
anthu onse akuyamikeni.
6 Lev. 26.4 Dziko lapansi lapereka zipatso zake,
Mulungu, Mulungu wathu adzatidalitsa.
7 Mas. 22.27 Mulungu adzatidalitsa;
ndipo malekezero onse a dziko lapansi adzamuopa Iye.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.