AKOLOSE 4 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1 Aef. 6.9 Ambuye inu, chitirani akapolo anu cholungama ndi cholingana; podziwa kuti inunso muli naye Mbuye mu Mwamba.

Awachenjeza za kupemphera ndi za kukhala nayo nzeru

2 Luk. 18.1 Chitani khama m'kupemphera, nimudikire momwemo ndi chiyamiko;

3Aef. 6.18-19ndi kutipempherera ifenso pomwepo, kuti Mulungu atitsegulire ife pakhomo pa mau, kuti tilankhule chinsinsi cha Khristu; chimenenso ndikhalira m'ndende,

4kuti ndichionetse ichi monga ndiyenera kulankhula.

51Ate. 4.12Muyendere munzeru ndi iwo akunja, kuchita machawi nthawi ingatayike.

6Mrk. 9.50Mau anu akhale m'chisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.

Atumidwa Tikiko ndi Onesimo

7 Aef. 6.21-22 Zonse za kwa ine adzakuzindikiritsani Tikiko, mbale wokondedwa ndi mtumiki wokhulupirika ndi kapolo mnzanga mwa Ambuye:

8Aef. 6.21-22amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichi chomwe, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti atonthoze mitima yanu;

9File. 10pamodzi ndi Onesimo, mbale wokhulupirika ndi wokondedwa, amene ali wa kwa inu. Zonse za kuno adzakuzindikiritsani inu.

Malonje

10 Mac. 15.22, 37; 19.29 Aristariko wam'ndende mnzanga akupatsani moni, ndi Marko, msuweni wa Barnabasi (amene munalandira zolamulira za kwa iye; akafika kwanu, mumlandire iye),

11ndi Yesu, wotchedwa Yusto, ndiwo a mdulidwe; iwo okha ndiwo antchito anzanga a mu Ufumu wa Mulungu, ndiwo akundikhalira ine chonditonthoza mtima.

12Mat. 5.48; Aro. 15.30; Akol. 1.7Akupatsani moni Epafra ndiye wa kwa inu, ndiye kapolo wa Khristu Yesu, wakulimbika m'mapemphero ake masiku onse chifukwa cha inu, kuti mukaime amphumphu ndi odzazidwa m'chifuniro chonse cha Mulungu.

13Pakuti ndimchitira iye umboni kuti adziwawitsa nayo ntchito chifukwa cha inu, ndi iwo a mu Laodikea, ndi iwo a mu Hierapoli.

142Tim. 4.10-11Akupatsani moni Luka sing'anga wokondedwa, ndi Dema.

15Aro. 16.5Perekani moni kwa abalewo a mu Laodikea, ndi Nimfa, ndi Mpingowo wa m'nyumba yao.

161Ate. 5.27Ndipo pamene mudamwerenga kalata iyi, amwerengenso mu Mpingo wa ku Laodikea, ndi inunso muwerenge wa ku Laodikea.

171Tim. 4.6Ndipo nenani kwa Arkipo, Samaliratu utumiki umene udaulandira mwa Ambuye, kuti uukwanitse.

18 1Ako. 16.21; Aheb. 13.3 Ndipereka moni ndi dzanja langa, kwa ine Paulo. Kumbukirani zomangira zanga. Chisomo chikhale nanu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help