2 TIMOTEO 2 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1 Aef. 6.10 Ndipo iwe, mwana wanga, limbika m'chisomo cha mwa Khristu Yesu.

22Tim. 1.13Ndipo zimene wazimva kwa ine mwa mboni zambiri, zomwezi uikize kwa anthu okhulupirika, amene adzadziwa kuphunzitsa enanso.

31Tim. 1.18Umve zowawa pamodzi nane monga msilikali wabwino wa Khristu Yesu.

4Msilikali sakodwa nazo ntchito wamba, kuti akakondweretse iye amene adamlemba usilikali.

51Ako. 9.25-26Koma ngatinso wina ayesana nao m'makani amasewero, samveka korona ngati sanayesane monga adapangana.

61Ako. 9.10Wam'munda wogwiritsitsa ntchitoyo ayenera akhale woyamba kulandira zipatsozo.

7Lingirira chimene ndinena; pakuti Ambuye adzakupatsa chidziwitso m'zonse.

81Ako. 15.1, 4, 20Kumbukira Yesu Khristu, wouka kwa akufa, wochokera m'mbeu ya Davide, monga mwa Uthenga Wabwino wanga;

9Mac. 9.16; 2Tim. 1.12m'menemo ndimva zowawa kufikira zomangira, monga wochita zoipa; koma mau a Mulungu samangika.

10Akol. 1.24Mwa ichi ndipirira zonse, chifukwa cha osankhika, kuti iwonso akapeze chipulumutsocho cha mwa Khristu Yesu, pamodzi ndi ulemerero wosatha.

11Aro. 6.5, 8Okhulupirika mauwa: Pakuti ngati tidamwalira ndi Iye, tidzakhalanso moyo ndi Iye:

12Mat. 10.33; Aro. 8.17ngati tipirira, tidzachitanso ufumu ndi Iye: ngati timkana Iye, Iyeyunso adzatikana ife:

13Num. 23.19; Aro. 3.3ngati tikhala osakhulupirika, Iyeyu akhala wokhulupirika; pakuti sangathe kudzikana yekha.

Umo azichita ndi osochera

14 1Tim. 6.4 Uwakumbutse izi, ndi kuwachitira umboni pamaso pa Ambuye, kuti asachite makani ndi mau osapindulitsa kanthu, koma ogwetsa iwo akumva.

15Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nao bwino mau a choonadi.

161Tim. 6.20Koma pewa nkhani zopanda pake; pakuti adzapitirira kutsata chisapembedzo,

171Tim. 1.20ndipo mau ao adzanyeka chilonda; a iwo ali Himeneo ndi Fileto;

181Ako. 15.12ndiwo amene adasokera kunena za choonadi, ponena kuti kuuka kwa akufa kwachitika kale, napasula chikhulupiriro cha ena.

19Nah. 1.7; Mat. 24.24Koma ndithu maziko a Mulungu aimika pokhazikika, ndi kukhala nacho chizindikiro ichi, Ambuye azindikira iwo amene ali ake; ndipo, Adzipatule kwa chosalungama yense wakutchula dzina la Ambuye.

20Aro. 9.21Koma m'nyumba yaikulu simuli zotengera za golide ndi siliva zokha, komatunso za mtengo ndi dothi; ndipo zina zaulemu, koma zina zopanda ulemu.

21Yes. 52.11; 2Tim. 1.18Ngati tsono munthu adziyeretsa yekha pa izi, adzakhala chotengera cha kuulemu, chopatulidwa, choyenera kuchita nacho Mbuye, chokonzera ntchito yonse yabwino.

221Tim. 6.11Koma thawa zilakolako za unyamata, nutsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera.

23Tit. 3.9Koma mafunso opusa ndi opanda malango upewe, podziwa kuti abala ndeu.

24Tit. 3.2Ndipo kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndeu, komatu akhale woyenera, waulere pa onse, wodziwa kuphunzitsa, woleza,

25Mac. 8.22; 1Pet. 3.15wolangiza iwo akutsutsana mofatsa; ngati kapena Mulungu awapatse iwo chitembenuziro, kukazindikira choonadi,

26Aro. 15.4ndipo akadzipulumutse kumsampha wa mdierekezi, m'mene anagwidwa naye, kuchifuniro chake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help