1 MBIRI 3 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Adzukulu a Davide

1 2Sam. 3.2-5 Ana a Davide tsono ombadwira ku Hebroni: woyamba Aminoni wa Ahinowamu wa ku Yezireele, wachiwiri Daniele wa Abigaile wa ku Karimele,

2wachitatu Abisalomu mwana wa Maaka mwana wamkazi wa Talimai mfumu ya Gesuri, wachinai Adoniya mwana wa Hagiti,

3wachisanu Sefatiya wa Abitala, wachisanu ndi chimodzi Itireamu wa mkazi wake Egila.

42Sam. 2.11; 5.5Anambadwira asanu ndi mmodzi mu Hebroni; ndi pomwepo anakhala mfumu zaka zisanu ndi ziwiri, ndi miyezi isanu ndi iwiri; ndi mu Yerusalemu anakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu zitatu.

52Sam. 5.14-16Ndipo ombadwira mu Yerusalemu ndi awa: Simea, ndi Sobabu, ndi Natani, ndi Solomoni, anai a Batisuwa mwana wamkazi wa Amiyele;

6ndi Ibara, ndi Elisama, ndi Elifeleti,

7ndi Noga, ndi Nefegi, ndi Yafiya,

8ndi Elisama, ndi Eliyada, ndi Elifeleti, asanu ndi anai.

9Onsewa ndiwo ana a Davide, pamodzi ndi ana a akazi aang'ono; ndipo Tamara ndiye mlongo wao.

101Maf. 1.15Ndipo mwana wa Solomoni ndiye Rehobowamu, Abiya mwana wake, Asa mwana wake, Yehosafati mwana wake,

112Maf. 8.16Yoramu mwana wake, Ahaziya mwana wake, Yowasi mwana wake,

12Amaziya mwana wake, Azariya mwana wake, Yotamu mwana wake,

13Ahazi mwana wake, Hezekiya mwana wake, Manase mwana wake,

14Amoni mwana wake, Yosiya mwana wake.

15Ndi ana a Yosiya: woyamba Yohanani, wachiwiri Yehoyakimu, wachitatu Zedekiya, wachinai Salumu.

16Ndi ana a Yehoyakimu: Yekoniya mwana wake, Zedekiya mwana wake.

17Ndi mwana wa Yekoniya: Asiri, Sealatiele mwana wake,

18ndi Malikiramu, ndi Pedaya, ndi Senazara, Yekamiya, Hosama, Nedabiya.

19Ezr. 2.2Ndi ana a Pedaya: Zerubabele ndi Simei; ndi ana a Zerubabele: Mesulamu, ndi Hananiya; ndipo Selomiti ndiye mlongo wao,

20ndi Hasuba, ndi Ohele, ndi Berekiya, ndi Hasadiya, ndi Yusabu-hesede; asanu.

21Ndi ana a Hananiya: Pelatiya, ndi Yesaya, ana a Refaya, ana a Arinani, ana a Obadiya, ana a Sekaniya.

22Ndi mwana wa Sekaniya: Semaya; ndi ana a Semaya: Hatusi, ndi Igala, ndi Bariya, ndi Neariya, ndi Safati; asanu ndi mmodzi.

23Ndi ana a Neariya: Eliyoenai, ndi Hizikiya, ndi Azirikamu, atatu.

24Ndi ana a Eliyoenai: Hodaviya, ndi Eliyasibu, ndi Pelaya, ndi Akubu, ndi Yohanani, ndi Delaya, ndi Anani, asanu ndi awiri.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help