YEREMIYA 48 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Chitsutso cha Mowabu

1 Yes. 15—16 Deut. 32.49 Za Mowabu. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Tsoka Nebo! Pakuti wapasuka; Kiriyataimu wachitidwa manyazi, wagwidwa; linga la pamtunda lachitidwa manyazi lapasudwa.

2Palibenso kutamanda Mowabu; mu Hesiboni anamlingiririra zoipa, ndi kuti, Tiyeni, tiwathe asakhalenso mtundu wa anthu. Iwenso, Madimeni, udzatontholetsedwa, lupanga lidzakulondola iwe.

3Mau amveka kuchokera ku Horonaimu, kufunkha ndi kuononga kwakukulu!

4Mowabu waonongedwa; ang'ono ake amveketsa kulira.

5Pakuti adzakwera pa chikweza cha Luhiti ndi kulira kosaleka; pakuti pa chitsiko cha Horonaimu amva kulira kowawa kwa chionongeko.

6Thawani, pulumutsani miyoyo yanu, mukhale amaliseche m'chipululu.

7Num. 21.29Pakuti, chifukwa wakhulupirira ntchito zanu ndi chuma chanu, iwenso udzagwidwa; ndipo Kemosi adza kundende, ansembe ake ndi akulu ake pamodzi.

8Ndipo wakufunkha adzafikira pa mizinda yonse, sudzapulumuka mzinda uliwonse; chigwa chomwe chidzasakazidwa, ndipo chidikha chidzaonongedwa; monga wanena Yehova.

9Patsani Mowabu mapiko, kuti athawe apulumuke; mizinda yake ikhale bwinja, lopanda wokhalamo.

101Sam. 15.9Atembereredwe iye amene agwira ntchito ya Yehova monyenga, atembereredwe iye amene abweza lupanga lake kumwazi.

11Zef. 1.12Mowabu wakhala m'mtendere kuyambira ubwana wake, wakhala pansenga, osatetekulidwa, sananke kundende; chifukwa chake makoleredwe ake alimobe mwa iye, fungo lake silinasinthike.

12Chifukwa chake, taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzatuma kwa iye otsanula, amene adzamtsanula iye; adzataya za mbiya zake, nadzaswa zipanda zao.

13Amo. 1.6-8Ndipo Mowabu adzachita manyazi chifukwa cha Kemosi, monga nyumba ya Israele inachita manyazi chifukwa cha Betele amene anamkhulupirira.

14Muti bwanji, Tili amphamvu, olimba mtima ankhondo?

15Yer. 46.18Mowabu wapasuka, akwera kulowa m'mizinda yake, ndi anyamata ake osankhika atsikira kukaphedwa, ati Mfumu, dzina lake ndiye Yehova wa makamu.

16Tsoka la Mowabu layandikira kudza, nsautso yake ifulumiratu.

17Inu nonse akumzungulira, mumchitire iye chisoni, inu nonse akudziwa dzina lake; muti, Chibonga cholimba chathyokatu, ndodo yokoma!

18Iwe mwana wamkazi wokhala mu Diboni, utsike pa ulemerero wako, nukhale ndi ludzu; pakuti wakufunkha Mowabu wakukwerera, iwe waononga malinga ako.

19Iwe wokhala mu Aroere, ima panjira, nusuzumire umfunse iye amene athawa, ndi mkazi amene apulumuka; nuti, Chachitidwa chiyani?

20Mowabu wachitidwa manyazi, pakuti wathyoka; kuwa nulire, nunene mu Arinoni, kuti Mowabu wapasuka.

21Chiweruzo chafika padziko lachidikha; pa Holoni, ndi pa Yahazi, ndi pa Mefaati;

22ndi pa Diboni, ndi pa Nebo, ndi pa Betedibilataimu;

23ndi pa Kiriyataimu, ndi pa Betegamuli, ndi pa Betemeoni;

24ndi pa Keriyoti, ndi pa Bozira, ndi pa mizinda yonse ya dziko la Mowabu, yakutali kapena yakufupi.

25Mas. 75.10Nyanga ya Mowabu yaduka, ndipo wathyoka mkono wake, ati Yehova.

26Yer. 48.42Umledzeretse iye; pakuti anadzikuza pokana Yehova; Mowabu yemwe adzamvimvinika m'kusanza kwake, ndipo iye adzasekedwanso.

27Zef. 2.8Kodi sunaseke Israele? Kodi iye anapezedwa mwa mbala? Pakuti nthawi zonse unena za iye, upukusa mutu.

28Inu okhala mu Mowabu, siyani mizinda, khalani m'thanthwe; nimukhale monga njiwa imene isanja chisanja chake pambali pakamwa pa dzenje.

29Ife tamva kudzikuza kwa Mowabu, wadzikuza ndithu, kunyang'wa kwake, ndi kunyada kwake, ndi kudzitama kwake, ndi kudzikuza kwa mtima wake.

30Ine ndidziwa mkwiyo wake, ati Yehova, kuti uli chabe; zonyenga zake sizinachite kanthu.

31Chifukwa chake ndidzakuwira Mowabu; inde, ndidzafuulira Mowabu yense, adzalirira anthu a ku Kiriheresi.

32Iwe mpesa wa Sibima; ndidzakulirira iwe ndi kulira kopambana kulira kwa Yazere, nthambi zako zinapitirira nyanja, zinafikira kunyanja ya Yazere; wakufunkha wagwera zipatso zako za mphakasa ndi mphesa zako.

33Yow. 1.12Ndipo kusekera ndi kukondwa kwachotsedwa, kumunda wobala ndi kudziko la Mowabu; ndipo ndaletsa vinyo pa zoponderamo; sadzaponda ndi kufuula; kufuula sikudzakhala kufuula.

34Kuyambira kufuula kwa Hesiboni mpaka ku Eleyale, mpaka ku Yahazi anakweza mau, kuyambira pa Zowari mpaka ku Horonaimu, ku Egilati-Selisiya; pakuti pamadzi a ku Nimurimu komwe padzakhala mabwinja.

35Ndiponso ndidzaletsa mu Mowabu, ati Yehova, iye amene apereka nsembe pamsanje, ndi iye amene afukizira milungu yake.

36Chifukwa chake mtima wanga umlirira Mowabu monga zitoliro, ndipo mtima wanga uwalirira anthu a Kiriheresi monga zitoliro, chifukwa chake zakuchuluka zake adadzionera zatayika.

37Pakuti mitu yonse ili yadazi, ndipo ndevu zili zometedwa; pa manja onse pali pochekedwachekedwa, ndi pachiuno chiguduli.

38Pamwamba pa matsindwi a Mowabu ndi m'miseu mwake muli kulira monsemonse; pakuti ndaswa Mowabu monga mbiya m'mene mulibe chikondwero, ati Yehova.

39Yasweka bwanji! Akuwa bwanji Mowabu! Wapotoloka bwanji ndi manyazi! Chomwecho Mowabu adzakhala choseketsa ndi choopsera onse omzungilira iye.

40Pakuti Yehova atero: Taonani, adzauluka ngati chiombankhanga, adzamtambasulira Mowabu mapiko ake.

41Keriyoti walandidwa, ndi malinga agwidwa, ndipo tsiku lomwelo mtima wa anthu amphamvu a Mowabu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.

42Ndipo Mowabu adzaonongeka asakhalenso mtundu wa anthu, chifukwa anadzikuzira yekha pa Yehova.

43Mantha, ndi dzenje, ndi khwekhwe, zili pa iwe, wokhala mu Mowabu, ati Yehova.

44Ndipo iye wakuthawa chifukwa cha mantha adzagwa m'dzenje; ndi iye amene atuluka m'dzenje adzagwidwa m'khwekhwe; pakuti ndidzatengera pa iye, pa Mowabu, chaka cha kulangidwa kwao, ati Yehova.

45Num. 21.28-29; 24.17Iwo amene anathawa aima opanda mphamvu pansi pamthunzi wa Hesiboni; pakuti moto watuluka mu Hesiboni, ndi malawi a moto m'kati mwa Sihoni, nadya ngodya ya Mowabu, ndi pakati pamutu pa ana a phokoso.

46Num. 21.28-29; 24.17Tsoka iwe, Mowabu! Anthu a Kemosi athedwa; pakuti ana ako aamuna atengedwa ndende, ndi ana ako aakazi atengedwa ndende.

47Koma ndidzabwezanso undende wa Mowabu masiku akumaliza, ati Yehova. Ziweruzo za Mowabu ndi zomwezi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help