1 AKORINTO 12 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Mphatso za Mzimu zisiyana

1 1Ako. 14.1 Koma za mphatso zauzimu, abale, sindifuna kuti mukhale osadziwa.

2Aef. 2.11-12Mudziwa kuti pamene munali amitundu, munatengedwa kunka kwa mafano aja osalankhula, monga munatsogozedwa.

3Mat. 16.17; 1Yoh. 4.2-3Chifukwa chake ndikuuzani inu, kuti palibe munthu wakulankhula mwa Mzimu wa Mulungu, anena, Yesu ngwotembereredwa; ndipo palibe wina akhoza kunena, Yesu ali Ambuye, koma mwa Mzimu Woyera.

4 Aro. 12.4-5 Ndipo pali mphatso zosiyana, koma Mzimu yemweyo.

5Aro. 12.6-8Ndipo pali mautumiki osiyana, koma Ambuye yemweyo.

6Ndipo pali machitidwe osiyana, koma Mulungu yemweyo, wakuchita zinthu zonse mwa onse.

7Aro. 12.6-8Koma kwa yense kwapatsidwa maonekedwe a Mzimu kuti apindule nao.

81Ako. 2.6-7Pakuti kwa mmodzi kwapatsidwa mwa Mzimu mau a nzeru; koma kwa mnzake mau a chidziwitso, monga mwa Mzimu yemweyo:

9Mat. 17.19-20kwa wina chikhulupiriro, mwa Mzimu yemweyo; ndi kwa wina mphatso za machiritso, mwa Mzimu mmodziyo;

10Mrk. 16.17ndi kwa wina machitidwe a mphamvu; ndi kwa wina chinenero; ndi kwa wina chizindikiro cha mizimu; kwa wina malilime a mitundumitundu; ndi kwa wina mamasulidwe a malilime.

11Aro. 12.4-8Koma zonse izi achita Mzimu mmodzi yemweyo, nagawira yense pa yekha monga afuna.

Thupi ndi limodzi, zingakhale ziwalo zisiyana

12Pakuti monga thupi lili limodzi, nilikhala nazo ziwalo zambiri; koma ziwalo zonse za thupilo, pokhala zambiri, zili thupi limodzi; momwemonso Khristu.

13Yoh. 7.37-39Pakutinso mwa Mzimu mmodzi ife tonse tinabatizidwa kulowa m'thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Agriki, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tinamwetsedwa Mzimu mmodzi.

14Pakutinso thupi silikhala chiwalo chimodzi, koma zambiri.

15Ngati phazi likati, Popeza sindili dzanja, sindili wa thupi; kodi silili la thupi chifukwa cha ichi?

16Ndipo ngati khutu likati, Popeza sindili diso, sindili wa thupi; kodi silili la thupi chifukwa cha ichi?

17Ngati thupi lonse likadakhala diso, kukadakhala kuti kununkhiza?

181Ako. 12.28Koma tsopano, Mulungu anaika ziwalo zonsezo m'thupi, monga anafuna.

19Koma ngati zonse zikadakhala chiwalo chimodzi, likadakhala kuti thupi?

20Koma tsopano pali ziwalo zambiri, koma thupi limodzi.

21Ndipo diso silingathe kunena kwa dzanja, Sindikufuna iwe, kapenanso mutu kwa mapazi, Sindikufunani inu.

22Koma makamakatu ziwalozo zoyesedwa zofooka m'thupi, zifunika;

23ndipo zimene tiziyesa zochepa ulemu m'thupi, pa izi tiika ulemu wochuluka woposa; ndi zinthu zosakoma zikhala nacho chokometsera choposa.

24Koma zokoma zathu zilibe kusowa; koma Mulungu analumikizitsa thupi, napatsa ulemu wochuluka kwa chosowacho;

25kuti kusakhale chisiyano m'thupi; koma kuti ziwalo zifanane ndi kusamalana china ndi chinzake.

26Ndipo chingakhale chiwalo chimodzi chimva chowawa, ziwalo zonse zimva pamodzi; chingakhale chimodzi chilemekezedwa, ziwalo zonse zikondwera nacho pamodzi.

27Aef. 1.23; 4.12; 5.23, 30Koma inu ndinu thupi la Khristu, ndi ziwalo, yense pa yekha.

281Ako. 12.18; Aef. 4.11Ndipotu Mulungu anaika ena mu Mpingo, poyamba atumwi, achiwiri aneneri, achitatu aphunzitsi, pamenepo zozizwa, pomwepo mphatso za machiritso, mathandizo, maweruziro, malilime a mitundumitundu.

29Kodi ali onse atumwi? Ali aneneri onse kodi? Ali aphunzitsi onse? Ali onse ochita zozizwa?

30Ali nazo mphatso za machiritso onse kodi? Kodi onse alankhula ndi malilime? Kodi onse amasulira mau?

311Ako. 14.39Koma funitsitsani mphatso zoposa. Ndipo ndikuonetsani njira yokoma yoposatu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help