AFILIPI 1 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1 1Ako. 1.2 Paulo ndi Timoteo, akapolo a Yesu Khristu, kwa oyera mtima onse mwa Khristu Yesu, akukhala ku Filipi, pamodzi ndi oyang'anira ndi atumiki:

2Aro. 1.7Chisomo kwa inu ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.

Chikondi cha Paulo cha pa Afilipi. Zipatso za undende wake

3 Aro. 1.8-9 Ndiyamika Mulungu wanga pokumbukira inu ponse;

4nthawi zonse m'pembedzero langa lonse la kwa inu nonse ndichita pembedzerolo ndi kukondwera,

5Afi. 4.15chifukwa cha chiyanjano chanu chakuthandizira Uthenga Wabwino, kuyambira tsiku loyambalo, kufikira tsopano lino;

61Ate. 5.24pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;

7Afi. 4.14monga kundiyenera ine kuyesa za inu nonse, popeza ndili nako m'mtima mwanga, kuti inu m'zomangira zanga, ndipo m'chodzikanira, ndi matsimikizidwe a Uthenga Wabwino, inu nonse muli oyanjana nane m'chisomo.

8Afi. 4.1Pakuti Mulungu ali mboni yanga, kuti ndilakalaka inu nonse m'phamphu la mwa Khristu Yesu.

91Ate. 3.12Ndipo ichi ndipempha, kuti chikondi chanu chisefukire chionjezere, m'chidziwitso, ndi kuzindikira konse;

10Mac. 24.16kuti mukayese inu zinthu zosiyana; kuti mukakhale a mtima woona ndi wosalakwa, kufikira tsiku la Khristu;

11Yoh. 15.4-5, 8odzala nacho chipatso cha chilungamo, chimene chili mwa Yesu Khristu, kuchitira Mulungu ulemerero ndi chiyamiko.

12Koma abale, ndifuna kuti muzindikire kuti zija za kwa ine zidachita makamaka kuthandizira Uthenga Wabwino;

13Afi. 4.22kotero kuti zomangira zanga zinaonekera mwa Khristu m'bwalo lonse la alonda, ndi kwa ena onse;

14ndi kuti unyinji wa abale mwa Ambuye, pokhulupirira m'zomangira zanga, alimbika mtima koposa kulankhula mau a Mulungu opanda mantha.

15Enatu alalikiranso Khristu chifukwa cha kaduka ndi ndeu; koma enanso chifukwa cha kukoma mtima;

16ena atero ndi chikondi, podziwa kuti anandiika ndichite chokanira cha Uthenga Wabwino;

17koma ena alalikira Khristu mochokera m'chotetana, kosati koona, akuyesa kuti adzandibukitsira chisautso m'zomangira zanga.

18Potero nchiyani? Chokhacho kuti monsemo, ngati pamaso pokha, ngati m'choonadi, Khristu alalikidwa; ndipo m'menemo ndikondwera, komanso ndidzakondwera.

19Aro. 8.9; 2Ako. 1.11Pakuti ndidziwa kuti ichi chidzandichitira ine chipulumutso, mwa pembedzero lanu ndi mwa kundipatsako kwa Mzimu wa Yesu Khristu;

20Aef. 6.19-20monga mwa kulingiriritsa ndi chiyembekezo changa, kuti palibe chinthu chidzandichititsa manyazi, komatu mwa kulimbika mtima konse, monga nthawi yonse, tsopanonso Khristu adzakuzidwa m'thupi langa, kapena mwa moyo, kapena mwa imfa.

21Pakuti kwa ine kukhala ndi moyo ndiko Khristu, ndi kufa kuli kupindula.

22Koma ngati kukhala ndi moyo m'thupi ndiko chipatso cha ntchito yanga, sindizindikiranso chimene ndidzasankha.

232Ako. 5.8; 2Tim. 4.6Koma ndipanidwa nazo ziwirizi, pokhala nacho cholakalaka cha kuchoka kukhala ndi Khristu, ndiko kwabwino koposaposatu;

24koma kukhalabe m'thupi ndiko kufunika koposa, chifukwa cha inu.

25Ndipo pokhulupirira pamenepo ndidziwa kuti ndidzakhala, ndi kukhalitsa ndi inu nonse, kuonjezera chimwemwe cha chikhulupiriro chanu;

262Ako. 1.14kuti kudzitamandira kwanu kuchuluke mu Khristu Yesu mwa ine, mwa kukhalanso ine kwa inu.

Akhristu alimbike, ayanjane, adzichepetse, atsate kuyeramtima

27 Aef. 4.1; Afi. 4.22; Yud. 3 Chokhachi, mayendedwe anu ayenere Uthenga Wabwino wa Khristu: kuti, ndingakhale nditi ndilinkudza ndi kuona inu, ndingakhale nditi ndili kwina, ndikamva za kwa inu, kuti muchilimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino;

282Ate. 1.5osaopa adani m'kanthu konse, chimene chili kwa iwowa chisonyezo cha chionongeko, koma kwa inu cha chipulumutso, ndicho cha kwa Mulungu;

29Mac. 5.41kuti kwapatsidwa kwa inu kwaufulu chifukwa cha Khristu, si kukhulupirira kwa Iye kokha, komatunso kumva zowawa chifukwa cha Iye,

30Mac. 16.19-39ndi kukhala nacho inu chilimbano chomwechi mudachiona mwa ine, nimukumva tsopano chili mwa ine.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help