EZEKIELE 14 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Chilango cha pa opembedza mafano

1Pamenepo anafika kwa ine akulu ena a Israele nakhala pansi pamaso panga.

2Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

32Maf. 3.13Wobadwa ndi munthu iwe, anthu awa anautsa mafano ao mumtima mwao, naimika chokhumudwitsa cha mphulupulu yao pamaso pao; ndifunsidwe nao konse kodi?

4Chifukwa chake ulankhule nao, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Aliyense wa nyumba ya Israele wakuutsa mafano ake mumtima mwake, naimika chokhumudwitsa cha mphulupulu yake pamaso pake, nadza kwa mneneri, Ine Yehova ndidzamyankhapo monga mwa mafano ake aunyinji;

5Yes. 1.4kuti ndigwire nyumba ya Israele mumtima mwao; popeza onsewo asanduka alendo ndi Ine mwa mafano ao.

6Chifukwa chake uziti kwa nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Bwerani, lekani mafano anu, tembenuzani nkhope zanu kuzisiya zonyansa zanu zonse.

7Pakuti aliyense wa nyumba ya Israele, kapena wa alendo ogonera mu Israele, wodzisiyanitsa kusatsata Ine, nautsa mafano ake m'mtima mwake, naimika chokhumudwitsa cha mphulupulu yake pamaso pake, nadzera mneneri kudzifunsira kwa Ine, Ine Yehova ndidzamyankha ndekha;

8Num. 26.10; Yer. 44.11ndipo ndidzaikira munthu uyu nkhope yanga imtsutse, ndi kumuyesa chodabwitsa, ndi chizindikiro, ndi mwambi, ndi kumsadza pakati pa anthu anga; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

91Maf. 22.23Ndipo akacheteka mneneriyo, nakanena mau, Ine Yehova ndamcheta mneneri uja; ndipo ndidzamtambasulira dzanja langa, ndi kumuononga pakati pa anthu anga Israele.

10Ndipo adzasenza mphulupulu yao, mphulupulu ya mneneri idzanga mphulupulu ya uja wamfunsira;

11Ezk. 11.20kuti nyumba ya Israele isasocherenso kusatsata Ine, kapena kudzidetsanso ndi zolakwa zao zonse; koma kuti akhale anthu anga, ndipo ndikhale Ine Mulungu wao, ati Ambuye Yehova.

Malango a Mulungu ali olungama

12Ndipo anandidzera mau a Yehova akuti,

13Yes. 3.1Likandichimwira dziko ndi kuchita monyenga, ndipo ndikalitambasulira dzanja langa, ndi kulithyolera mchirikizo wake, ndiwo mkate, ndi kulitumizira njala, ndi kulidulira munthu ndi nyama,

14Yer. 15.1chinkana akadakhala m'mwemo anthu awa atatu, Nowa, Daniele, ndi Yobu, akadapulumutsa moyo wao wokha mwa chilungamo chao, ati Ambuye Yehova.

15Ndikapititsa zilombo zoipa pakati padziko, ndi kupulula ana, kuti likhale lachipululu losapitako munthu chifukwa cha zilombo,

16Ezk. 14.14chinkana anthu omwewo atatu akadakhala m'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana aamuna kapena aakazi; iwo akadapulumuka okha; koma dziko likadakhala lachipululu.

17Kapena ndikadza padziko ndi lupanga, ndi kuti, Lupanga lipite pakati padziko, kuti ndilidulire munthu ndi nyama;

18Ezk. 14.14chinkana anthu atatuwo akadakhala m'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana aamuna kapena aakazi; koma iwo akadapulumuka okha.

192Sam. 24.15Kapena ndikatumizira dzikolo mliri, ndi kulitsanulira ukali wanga ndi mwazi, kulidulira munthu ndi nyama;

20Ezk. 14.14chinkana Nowa, Daniele, ndi Yobu, akadakhala m'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana aamuna kapena aakazi; akadapulumutsa moyo wao wokha ndi chilungamo chao.

21Ezk. 5.17Pakuti atero Ambuye Yehova, Kopambana kotani nanga ndikatumizira Yerusalemu maweruzo anga anai owawa, lupanga, njala, zilombo zoipa, ndi mliri, kuudulira anthu ndi nyama?

22Ezk. 6.8Koma onani mudzatsala opulumuka m'mwemo amene adzatulutsidwa, ndiwo ana aamuna ndi aakazi; taonani, adzatuluka kudza kwa inu; ndipo mudzaona njira zao, ndi zochita zao; mudzatonthozedwanso pa zoipa ndazitengera pa Yerusalemu, inde pa zonse ndazitengerapo.

23Yer. 22.8-9Ndipo adzakusangalatsani pamene muona njira yao, ndi zochita zao; ndipo mudzadziwa kuti sindinazichite kopanda chifukwa zonse ndinazichita momwemo, ati Ambuye Yehova.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help