MASALIMO 102 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Wopsinjika apempha Mulungu achitire anthu ake chifundo, amitundu nammverensoPemphero la Wozunzika, m'mene anakomoka natsanulira cholingalira chake pamaso pa Yehova.

1Yehova, imvani pemphero langa,

ndipo mfuu wanga ufikire Inu.

2 Mas. 27.9 Musandibisire nkhope yanu tsiku la nsautso yanga;

munditchereze khutu lanu;

tsiku limene ndiitana ine mundiyankhe msanga.

3Popeza masiku anga akanganuka ngati utsi,

ndi mafupa anga anyeka ngati nkhuni.

4Mtima wanga ukunga udzu womweta, nufota;

popeza ndiiwala kudya mkate wanga.

5Chifukwa cha liu la kubuula kwanga

mnofu wanga umamatika kumafupa anga.

6Ndikunga vuwo m'chipululu;

ndikhala ngati kadzidzi wa kumabwinja.

7Ndidikira, ndikhala ngati mbalame

ili yokha pamwamba pa tsindwi.

8Adani anga anditonza tsiku lonse;

akundiyalukirawo alumbirira ine.

9Pakuti ndadya mapulusa ngati mkate,

ndi kusakaniza chomwera changa ndi misozi,

10 Mas. 30.7 chifukwa cha ukali wanu ndi kuzaza kwanu;

popeza munandinyamula ndipo munandigwetsa.

11 Mas. 109.23; Yes. 40.6-8 Masiku anga akunga mthunzi womka m'tali;

ndipo ine ndauma ngati udzu.

12Koma Inu, Yehova, mukhalabe kunthawi yonse;

ndi chikumbukiro chanu ku mibadwomibadwo.

13 Yes. 60.10 Inu mudzauka, ndi kuchitira nsoni Ziyoni;

popeza yafika nyengo yakumchitira chifundo, nyengo yoikika.

14Pakuti atumiki anu akondwera nayo miyala yake,

nachitira chifundo fumbi lake.

15 1Maf. 8.43 Pamenepo amitundu adzaopa dzina la Yehova,

ndi mafumu onse a dziko lapansi ulemerero wanu.

16 Yes. 60.1-2 Pakuti Yehova anamanga Ziyoni,

anaoneka mu ulemerero wake;

17 Neh. 1.6, 11 anasamalira pemphero la iwo akusowa konse,

osapepula pemphero lao.

18 Aro. 15.4 Ichi adzachilembera mbadwo ukudza;

ndi mtundu wa anthu umene udalengedwa udzamlemekeza Yehova.

19Pakuti anapenya pansi ali kumwamba kuli malo ake opatulika;

Yehova pokhala kumwamba anapenya dziko lapansi;

20 Mas. 79.11 kuti amve kubuula kwa wandende;

namasule ana a imfa.

21 Mas. 22.22 Kuti anthu alalikire dzina la Yehova mu Ziyoni,

ndi chilemekezo chake mu Yerusalemu;

22Posonkhana pamodzi mitundu ya anthu,

ndi maufumu kuti atumikire Yehova.

23Iye analanda mphamvu yanga panjira;

anachepsa masiku anga.

24 Yes. 38.10 Ndinati, Mulungu wanga, musandichotse pakati pa masiku anga:

Zaka zanu zikhalira m'mibadwomibadwo.

25 Gen. 1.1; 2.1; Aheb. 1.10-12 Munakhazika dziko lapansi kalelo;

ndipo zakumwamba ndizo ntchito ya manja anu.

26 Aheb. 1.10-12 Zidzatha izi, koma Inu mukhala:

Inde, zidzatha zonse ngati chovala;

mudzazisintha ngati malaya, ndipo zidzasinthika:

27 Mala. 3.6; Aheb. 13.8 Koma Inu ndinu yemweyo,

ndi zaka zanu sizifikira kutha.

28 Mas. 69.36 Ana a atumiki anu adzakhalitsa,

ndi mbeu zao zidzakhazikika pamaso panu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help