1 Eks. 15.1; Ower. 5.1 Ndipo Davide analankhula kwa Yehova mau a nyimbo iyi tsikuli Yehova anampulumutsa m'dzanja la adani ake onse, ndi m'dzanja la Saulo.
2Deut. 32.4; Mas. 18.2-50Ndipo anati,
Yehova ndiye thanthwe langa,
ndi ngaka yanga, ndi Mpulumutsi wanga, wangadi.
3 Gen. 15.1; Mas. 14.6; Miy. 18.10; Luk. 1.69; Aheb. 2.13 Mulungu wa thanthwe langa,
Iye ndidzamkhulupirira;
chikopa changa, ndi nyanga ya chipulumutso changa,
nsanja yanga yaitali, ndi populumukirapo panga;
Mpulumutsi wanga, mundipulumutsa kuchiwawa.
4Ndidzaitana kwa Yehova amene ayenera timtamande;
chomwecho ndidzapulumutsidwa kwa adani anga.
5 Mas. 32.6 Pakuti mafunde a imfa anandizinga,
mitsinje ya zopanda pake inandiopsa ine.
6Zingwe za kumanda zinandizingira;
misampha ya imfa inandifikira ine.
7 Eks. 3.7; Mas. 116.4 M'kusauka kwanga ndinaitana kwa Yehova,
inde ndinakuwira kwa Mulungu wanga;
ndipo Iye anamva mau anga ali mu Kachisi wake,
ndi kulira kwanga kunafika ku makutu ake.
8Pomwepo dziko linagwedezeka ndi kunthunthumira.
Maziko a dziko la kumwamba anasunthika.
Nagwedezeka, chifukwa Iye anakwiya.
9M'mphuno mwake munatuluka utsi,
ndi moto wotuluka m'kamwa mwake unaononga;
makala anayaka nao.
10Anaweramitsa miyambanso, natsika;
ndipo mdima wandiweyani unali pansi pa mapazi ake.
11Ndipo Iye anaberekeka pa kerubi nauluka;
inde anaoneka pa mapiko a mphepo.
12Ndipo anayesa mdimawo ngati mahema omzungulira Iye,
kusonkhana kwa madzi ndi mitambo yochindikira ya mlengalenga.
13Cheza cha pamaso pake
makala a moto anayaka.
14 Yes. 30.30 Yehova anagunda kumwamba;
ndipo Wam'mwambamwamba ananena mau ake.
15Ndipo Iye anatumiza mivi, nawawaza;
mphezi, nawaopsa.
16Pamenepo m'munsi mwa nyanja munaoneka,
maziko a dziko anaonekera poyera,
ndi mtonzo wa Yehova,
ndi mpumo wa mpweya wa m'mphuno mwake.
17Iye anatumiza kuchokera kumwamba nanditenga;
Iye ananditulutsa m'madzi aakulu.
18Iye anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,
kwa iwo akudana ndi ine;
pakuti anandiposa mphamvu.
19Anandifikira ine tsiku la tsoka langa;
koma Yehova anali mchirikizo wanga.
20 Mas. 22.8; 31.8 Iye ananditulutsanso ku malo aakulu;
Iye anandipulumutsa,
chifukwa akondwera ndi ine.
21 1Sam. 26.23 Yehova anandibwezera monga mwa cholungama changa;
monga mwa kuyera kwa manja anga anandipatsa mphotho.
22 Mas. 128.1 Pakuti ndinasunga njira za Yehova,
osapatukira ku zoipa kusiya Mulungu wanga.
23Pakuti maweruzo ake onse anali pamaso panga;
ndipo za malemba ake, sindinawapatukire.
24 Yob. 1.1 Ndinakhalanso wangwiro kwa Iye,
ndipo ndinadzisunga kusachita kuipa kwanga.
25 2Sam. 22.21 Chifukwa chake Yehova anandibwezera monga mwa cholungama changa;
monga mwa kuyera kwanga pamaso pake.
26 Mat. 5.7 Ndi chifundo Inu mudzadzionetsa wachifundo,
ndi munthu wangwiro mudzadzionetsa wangwiro.
27 Mas. 24.4; Mat. 5.8 Ndi oyera mtima mudzadzionetsa woyera mtima;
ndi otsutsatsutsa mudzadzionetsa wopotoza.
28 Eks. 3.7-8; Luk. 1.51-52 Ndipo mudzapulumutsa anthu osautsidwa;
koma maso anu ali pa odzikuza kuti muwachepetse.
29Pakuti Inu ndinu nyali yanga, Yehova;
ndipo Yehova adzaunika mumdima mwanga.
30Pakuti ndi Inu ndithamangira gulu;
ndi Mulungu wanga ndilumphira linga.
31 Dan. 4.37; Mat. 5.48 Kunena za Mulungu, njira yake ili yangwiro;
mau a Yehova anayesedwa;
Iye ndiye chikopa kwa onse akukhulupirira Iye.
32Pakuti Mulungu ndani, koma Yehova?
Ndipo thanthwe ndani, koma Mulungu wathu?
33 Mas. 89.26 Mulungu ndiye linga langa lamphamvu;
ndipo Iye ayendetsa angwiro mu njira yake.
34Iye asandutsa mapazi ake akunga mapazi a mbawala;
nandiika pa misanje yanga.
35Iye aphunzitsa manja anga nkhondo;
kotero kuti manja anga alifula uta wamkuwa.
36Ndiponso munandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu;
ndi kufatsa kwanu kunandikulitsa.
37Munakulitsa kulunza kwanga pansi panga,
ndi mapazi anga sanaterereke.
38Ndinapirikitsa adani anga, ndi kuwaononga;
ndiponso sindinabwerere mpaka nditawatha.
39Ndinawatha ndi kuwapyoza, kuti sangathe kuuka,
inde anagwa pansi pa mapazi anga.
40Pakuti Inu munandimanga m'chuuno ndi mphamvu ya kunkhondo;
munandigonjetsera akundiukira.
41Munatembenuzitsanso adani anga andipatse mbuyo,
kuti ndiwalikhe akudana ndi ine.
42Anayang'ana iwo, koma panalibe wopulumutsa;
ngakhale kwa Yehova, koma Iye sanawayankhe.
43Pomwepo ndinawasansantha asalale ngati fumbi la padziko,
ndinawapondereza ngati dothi la m'makwalala.
44 Deut. 28.13 Inunso munandipulumutsa ine pa kulimbana kwa anthu anga;
munandisunga ndikhale mutu wa amitundu;
Anthu amene sindinawadziwe adzanditumikira ine.
45Alendo adzandigonjera ine,
pakumva za ine, adzandimvera pomwepo.
46Alendo adzafota,
nadzabwera ndi kunthunthumira otuluka mokwiririka mwao.
47 Eks. 15.2 Yehova ali ndi moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa;
ndipo akulitsidwe Mulungu wa thanthwe la chipulumutso changa;
48inde Mulungu wakundibwezera chilango ine,
ndi kundigonjetsera anthu a mitundu.
49Amene anditulutsa kwa adani anga;
inde mundikweza ine pamwamba pa iwo akundiukira;
mundipulumutsa kwa munthu wachiwawa.
50 Aro. 15.9 Chifukwa chake ndidzakuongani Yehova, pakati pa amitundu,
ndipo ndidzaimba zolemekeza dzina lanu.
51 Mas. 89.20, 29 Iye apatsa mfumu yake chipulumutso chachikulu;
naonetsera chifundo wodzozedwa wake,
kwa Davide ndi mbeu yake ku nthawi zonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.