YOBU 22 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Elifazi amtchulira Yobu zoipa zambiri, namuuza alape, Mulungu nadzamchitira chifundo(22.1—27.23)

1Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha, nati,

2Kodi munthu apindulira Mulungu?

Koma wanzeru angodzipindulira yekha.

3Kodi Wamphamvuyonse akondwera nako

kuti iwe ndiwe wolungama?

Kapena kodi apindula nako kuti ukwaniritsa njira zako?

4Kodi akudzudzula, nadza nawe kumlandu,

chifukwa cha kumuopa kwako?

5Zoipa zako sizichuluka kodi?

Ndi mphulupulu zako sizikhala zosawerengeka kodi?

6 Eks. 22.26-27; Ezk. 18.12 Pakuti wamtenga chikole kwa mbale wako wopanda chifukwa,

ndi kuvula ausiwa zovala zao.

7 Yes. 58.6-7; Mat. 25.42 Sunampatsa wolema madzi amwe,

ndi wanjala unammana chakudya.

8Koma munthu mwini mphamvu, dziko ndi lake;

ndi munthu wovomerezeka, anakhala momwemo.

9 Yes. 10.1-2 Unabweza akazi amasiye osawaninkha kanthu,

ndi manja a ana amasiye anathyoledwa.

10Chifukwa chake misampha ikuzinga.

Ndi mantha akuvuta modzidzimutsa,

11kapena mdima kuti ungaone,

ndi madzi aunyinji akumiza.

12Kodi Mulungu sakhala m'mwamba m'tali?

Ndipo penyani kutalika kwake kwa nyenyezi, zili m'talitali.

13 Mas. 10.11 Ndipo ukuti, Adziwa chiyani Mulungu?

Aweruza kodi mwa mdima wa bii?

14 Mas. 139.11-12 Mitambo ndiyo chomphimba, kuti angaone;

ndipo amayenda pa thambo lakumwamba.

15Udzasunga kodi njira yakale,

anaiponda anthu amphulupulu?

16Amene anakwatulidwa isanafike nyengo yao,

chigumula chinakokolola kuzika kwao;

17amene anati kwa Mulungu, Tichokereni;

ndipo, Angatichitire chiyani Wamphamvuyonse?

18Angakhale Iye adadzaza nyumba zao ndi zabwino;

koma uphungu wa oipa unditalikira.

19Olungama achiona nakondwera;

ndi osalakwa awaseka pwepwete,

20ndi kuti, Zoonadi, otiukirawo alikhidwa,

ndi zowatsalira, moto unazipsereza.

21Uzolowerane ndi Iye, nukhale ndi mtendere;

ukatero zokoma zidzakudzera.

22 Mas. 119.11 Landira tsono chilamulo pakamwa pake,

nuwasunge maneno ake mumtima mwako.

23Ukabweranso kwa Wamphamvuyonse, udzamanga bwino;

ukachotsera chosalungama kutali kwa mahema ako.

24Ndipo utaye chuma chako kufumbi,

ndi golide wa ku Ofiri ku miyala ya kumitsinje.

25Ndipo Wamphamvuyonse adzakhala chuma chako,

ndi ndalama zako zofunika.

26 Yes. 58.14 Pakuti pamenepo udzakondwera naye Wamphamvuyonse,

ndi kuweramutsa nkhope yako kwa Mulungu.

27 Mas. 50.1, 15 Udzampemphera ndipo adzakumvera;

nudzatsiriza zowinda zako.

28Ukatsimikiza mtima kakuti, kadzakhazikikira iwe;

ndi kuunika kudzawala panjira zako.

29 Miy. 29.23; Yak. 4.6 Anthu akakugwetsa pansi, udzati, Adzandikweza;

ndipo adzapulumutsa wodzichepetsayo.

30Adzamasula ngakhale wopalamula,

inde adzamasuka mwa kuyera kwa manja ako.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help